-
2 Mbiri 33:2-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Iye ankachita zoipa pamaso pa Yehova ndipo ankatsatira zinthu zonyansa zomwe ankachita anthu a mitundu imene Yehova anaithamangitsa pamaso pa Aisiraeli.+ 3 Iye anamanganso malo okwezeka amene Hezekiya bambo ake anagwetsa.+ Anamanga maguwa ansembe a Abaala komanso mizati yopatulika,* ndipo ankagwadira gulu lonse la zinthu zakumwamba ndiponso kuzitumikira.+ 4 Anamanganso maguwa ansembe mʼnyumba ya Yehova,+ imene Yehova ananena kuti: “Dzina langa lidzakhala ku Yerusalemu mpaka kalekale.”+ 5 Iye anamanga maguwa ansembe a gulu lonse la zinthu zakumwamba mʼmabwalo awiri a nyumba ya Yehova.+ 6 Manase anatentha* ana ake aamuna pamoto+ mʼChigwa cha Mwana wa Hinomu,+ ankachita zamatsenga,+ ankawombeza, ankachita zanyanga ndiponso anaika anthu olankhula ndi mizimu ndi olosera zamʼtsogolo.+ Iye anachita zinthu zoipa kwambiri pamaso pa Yehova ndipo anamukwiyitsa.
-