105 Yamikani Yehova,+ itanani pa dzina lake,
Dziwitsani mitundu ya anthu ntchito zake.+
2 Muimbireni, muimbireni nyimbo zomutamanda,
Ganizirani mozama ntchito zake zonse zodabwitsa.+
3 Nyadirani dzina lake loyera.+
Mitima ya anthu ofunafuna Yehova isangalale.+
4 Funafunani Yehova+ ndipo muzidalira mphamvu zake.
Nthawi zonse muzimupempha kuti akuthandizeni.
5 Kumbukirani ntchito zodabwitsa zimene wachita,
Kumbukirani zozizwitsa zake ndi ziweruzo zimene wapereka,+
6 Inu mbadwa za Abulahamu mtumiki wake,+
Inu ana a Yakobo, osankhidwa ake.+