24 Mose atangomaliza kulemba mawu onse a Chilamulo ichi mʼbuku,+ 25 Mose analamula Alevi amene amanyamula likasa la pangano la Yehova kuti: 26 “Tengani buku ili la Chilamulo+ ndipo muliike pambali pa likasa+ la pangano la Yehova Mulungu wanu, ndipo lidzakhala mboni ya Mulungu yokutsutsani.