-
2 Mafumu 15:5-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Yehova anachititsa khate mfumuyo moti inali yakhate+ mpaka tsiku lomwe inamwalira. Inkakhala mʼnyumba kwayokha+ ndipo mwana wake Yotamu+ ndi amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu komanso kuweruza anthu amʼdzikolo.+ 6 Nkhani zina zokhudza Azariya+ komanso zonse zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda. 7 Kenako Azariya, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda a makolo ake+ mu Mzinda wa Davide. Ndiyeno Yotamu mwana wake anakhala mfumu mʼmalo mwake.
-