Genesis 16:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Ndiyeno Hagara anapemphera kwa Yehova* kuti: “Inu ndinu Mulungu amene amaona chilichonse.”+ Ananenanso kuti: “Kodi nanenso pano ndaona amene amatha kundionayo?” 2 Mbiri 16:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi+ kuti aonetse mphamvu zake* kwa anthu odzipereka ndi mtima wonse kwa iye.*+ Mwachita zopusa pa nkhani imeneyi. Kuyambira pano mʼdziko lanu muzichitika nkhondo.”+ Salimo 139:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Mumandiona* ndikamayenda komanso ndikagona.Mumadziwa chilichonse chimene ndikuchita.+ Miyambo 5:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Chifukwa maso a Yehova amaona chilichonse chimene munthu akuchita,Ndipo iye amafufuza njira zake zonse.+ Yeremiya 32:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Zolinga zanu ndi zazikulu ndipo zochita zanu ndi zamphamvu.+ Maso anu amaona zonse zimene anthu amachita,+ kuti munthu aliyense mumuchitire zinthu mogwirizana ndi njira zake komanso zochita zake.+
13 Ndiyeno Hagara anapemphera kwa Yehova* kuti: “Inu ndinu Mulungu amene amaona chilichonse.”+ Ananenanso kuti: “Kodi nanenso pano ndaona amene amatha kundionayo?”
9 Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi+ kuti aonetse mphamvu zake* kwa anthu odzipereka ndi mtima wonse kwa iye.*+ Mwachita zopusa pa nkhani imeneyi. Kuyambira pano mʼdziko lanu muzichitika nkhondo.”+
21 Chifukwa maso a Yehova amaona chilichonse chimene munthu akuchita,Ndipo iye amafufuza njira zake zonse.+
19 Zolinga zanu ndi zazikulu ndipo zochita zanu ndi zamphamvu.+ Maso anu amaona zonse zimene anthu amachita,+ kuti munthu aliyense mumuchitire zinthu mogwirizana ndi njira zake komanso zochita zake.+