-
1 Mafumu 19:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Choncho Eliya anachita mantha moti ananyamuka nʼkuyamba kuthawa kuti apulumutse moyo wake.+ Atafika ku Beere-seba+ wa ku Yuda,+ anasiya mtumiki wake kumeneko. 4 Ndipo iyeyo analowa mʼchipululu nʼkuyenda ulendo wa tsiku limodzi. Kenako anafika pa kamtengo kenakake nʼkukhala pansi pake. Ndiyeno anapempha kuti afe ponena kuti: “Basi ndatopa nazo. Tsopano chotsani moyo wanga Yehova,+ chifukwa siine woposa makolo anga.”
-
-
Yona 4:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Choncho iye anapemphera kwa Yehova kuti: “Inu Yehova, kodi zimene ndimaopa ndili kwathu zija si zimenezi? Nʼchifukwa chaketu ndinkafuna kuthawira ku Tarisi.+ Ndinadziwa kuti inu ndinu Mulungu wachifundo, wokoma mtima, wosakwiya msanga, wachikondi chokhulupirika chochuluka+ komanso mumamva chisoni mukafuna kubweretsa tsoka. 3 Inu Yehova, chotsani moyo wanga, chifukwa kuli bwino ndingofa kusiyana nʼkuti ndikhale ndi moyo.”+
-