Ekisodo 14:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Ine ndidzalola kuti Farao aumitse mtima wake,+ ndipo adzawathamangira. Ndidzalemekeza dzina langa pogonjetsa Farao ndi gulu lake lonse lankhondo,+ ndipo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”+ Choncho Aisiraeli anachitadi zomwezo. Yoswa 2:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Tinamva mmene Yehova anaphwetsera madzi a Nyanja Yofiira pamene munkachoka ku Iguputo.+ Komanso mmene munaphera mafumu awiri a Aamori, Sihoni+ ndi Ogi,+ kutsidya* kwa mtsinje wa Yorodano. 2 Mafumu 19:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Tsopano inu Yehova Mulungu wathu, chonde tipulumutseni mʼmanja mwake, kuti maufumu onse apadziko lapansi adziwe kuti inu nokha Yehova, ndinu Mulungu.”+
4 Ine ndidzalola kuti Farao aumitse mtima wake,+ ndipo adzawathamangira. Ndidzalemekeza dzina langa pogonjetsa Farao ndi gulu lake lonse lankhondo,+ ndipo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”+ Choncho Aisiraeli anachitadi zomwezo.
10 Tinamva mmene Yehova anaphwetsera madzi a Nyanja Yofiira pamene munkachoka ku Iguputo.+ Komanso mmene munaphera mafumu awiri a Aamori, Sihoni+ ndi Ogi,+ kutsidya* kwa mtsinje wa Yorodano.
19 Tsopano inu Yehova Mulungu wathu, chonde tipulumutseni mʼmanja mwake, kuti maufumu onse apadziko lapansi adziwe kuti inu nokha Yehova, ndinu Mulungu.”+