Yoswa
2 Tsopano Yoswa mwana wa Nuni anatuma amuna awiri mwachinsinsi kuchokera ku Sitimu+ kuti akafufuze zokhudza dziko la Kanani. Anawauza kuti: “Pitani mukafufuze zokhudza dzikolo, makamaka mzinda wa Yeriko.” Choncho iwo anapita nʼkukafika kunyumba kwa mayi wina dzina lake Rahabi,+ yemwe anali hule, ndipo anakhala kumeneko. 2 Kenako mfumu ya Yeriko inauzidwa kuti: “Kwabwera Aisiraeli usiku uno kudzafufuza zokhudza dzikoli.” 3 Mfumu ya Yeriko itamva zimenezi, inatumiza anthu kukauza Rahabi kuti: “Tulutsa amuna amene abwera kuno ndipo ali mʼnyumba mwako, chifukwa abwera kudzafufuza dziko lonseli.”
4 Koma mayiyo anatenga amuna awiriwo nʼkuwabisa. Kenako anayankha kuti: “Nʼzoona, amunawo anabweradi, koma sindinadziwe kuti achokera kuti. 5 Mmene kumada, nthawi yotseka geti itayandikira, amunawo anatuluka. Sindikudziwa kumene alowera. Athamangireni mwamsanga. Muwapeza amenewo.” 6 (Koma iye anali atapita nawo padenga, nʼkuwabisa pansi pa mapesi a fulakesi* omwe anali padengapo.) 7 Anthuwo anathamangira amuna aja cha kowolokera mtsinje wa Yorodano.+ Ndipo atangotuluka pageti la mzinda, nthawi yomweyo getilo linatsekedwa.
8 Amuna aja asanagone, Rahabi anakwera padengapo. 9 Ndipo anawauza kuti: “Ndikudziwa kuti Yehova akupatsani dzikoli+ ndipo tonse tikuchita nanu mantha.+ Aliyense mʼdzikoli mtima wake suli mʼmalo chifukwa cha inu.+ 10 Tinamva mmene Yehova anaphwetsera madzi a Nyanja Yofiira pamene munkachoka ku Iguputo.+ Komanso mmene munaphera mafumu awiri a Aamori, Sihoni+ ndi Ogi,+ kutsidya* kwa mtsinje wa Yorodano. 11 Titangomva zimenezi tinataya mtima,* ndipo chifukwa cha inu, palibe aliyense amene akulimba mtima. Ndithu, Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wakumwamba ndi dziko lapansi.+ 12 Tsopano, chonde lumbirani pamaso pa Yehova, kuti chifukwa choti ndakusonyezani chikondi chokhulupirika, inunso mudzasonyeze anthu a mʼbanja la bambo anga chikondi chokhulupirika, ndipo mundipatse chizindikiro chodalirika. 13 Musadzaphe bambo anga, mayi anga, azichimwene anga ndi azichemwali anga limodzi ndi mabanja awo. Mudzatisiye amoyo.”+
14 Amunawo anayankha kuti: “Tikadzapanda kusunga lonjezo lathu, ifeyo tidzafe mʼmalo mwa inu. Mukapanda kuulula nkhaniyi, Yehova akadzatipatsa dzikoli, ifenso tidzakusonyezani kukoma mtima* ndipo tidzakhala okhulupirika.” 15 Kenako mayiyo anawapatsa chingwe ndipo iwo anatulukira pawindo pogwiritsa ntchito chingwecho, chifukwa mpanda wa mzindawo unalinso khoma la nyumba yake. Tingoti khoma la nyumba yakeyo linali mbali ya mpandawo.+ 16 Iye anauza amunawo kuti: “Muthawire kumapiri kuti amene akukusakani aja asakupezeni. Mukabisale kumeneko masiku atatu, mpaka iwo atabwerako, kenako muzikapita kwanu.”
17 Amunawo anayankha kuti: “Tisungadi pangano limene watilumbiritsali, ndipo tidzakhala opanda mlandu+ 18 ngati pobwera tidzapeza utamangirira chingwe chofiirachi pawindo limene watitulutsirapoli. Uuze bambo ako, mayi ako, azichimwene ako, azichemwali ako ndi onse a mʼbanja la bambo ako kuti adzakhale mʼnyumba mwakomu.+ 19 Aliyense amene adzatuluke mʼnyumba yako kupita panja, magazi ake adzakhala pamutu pake ndipo ife tidzakhala opanda mlandu. Koma aliyense amene adzakhalebe nawe mʼnyumbamu akadzaphedwa, magazi ake adzakhala pamutu pathu. 20 Ndipo ngati ungaulule nkhaniyi,+ tidzakhalanso opanda mlandu pa pangano limene watilumbiritsali.” 21 Mayiyo anayankha kuti: “Zikhale momwemo.”
Atatero anawauza kuti azipita ndipo iwo ananyamuka. Kenako mayiyo anamanga chingwe chofiira chija pawindopo. 22 Choncho amuna aja anapita kumapiri ndipo anakhala kumeneko masiku atatu mpaka anthu owasakawo atabwerera. Owasakawo anali atawafunafuna mumsewu uliwonse, koma osawapeza. 23 Amuna awiri aja anachoka kumapiriko, ndipo anawoloka mtsinje nʼkukafika kwa Yoswa mwana wa Nuni. Atafika anamufotokozera zonse zimene zinawachitikira. 24 Iwo anauza Yoswa kuti: “Yehova wapereka dziko lonselo mʼmanja mwathu.+ Ndipo anthu onse a mʼdzikomo akuchita mantha chifukwa cha ife.”+