-
2 Samueli 19:25-27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Atafika* ku Yerusalemu kukakumana ndi mfumu, mfumuyo inamufunsa kuti: “Mefiboseti, nʼchifukwa chiyani sunapite nane?” 26 Iye anayankha kuti: “Mbuyanga mfumu, mtumiki wanga+ ndi amene anandipusitsa. Ine mtumiki wanu ndinamuuza kuti, ‘Ndiikireni chishalo pabulu ndikwerepo kuti ndipite limodzi ndi mfumu,’ chifukwa ine mtumiki wanu ndine wolumala.+ 27 Koma mtumiki wangayo anakuuzani inu mbuyanga mfumu+ zinthu zabodza zokhudza ine mtumiki wanu. Komabe inu mbuyanga muli ngati mngelo wa Mulungu woona, choncho chitani zilizonse zomwe mukuona kuti nʼzabwino.
-