1 Mafumu 2:44 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 44 Kenako mfumuyo inauza Simeyi kuti: “Iweyo ukudziwa mumtima mwako zoipa zonse zimene unachitira Davide bambo anga.+ Yehova akubwezera pamutu pako zoipa zimene unachita.+ 1 Mafumu 2:46 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 46 Ndiyeno mfumuyo inalamula Benaya mwana wa Yehoyada kuti aphe Simeyi ndipo anamuphadi.+ Choncho ufumu unakhazikika mʼmanja mwa Solomo.+ Miyambo 20:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Kukhulupirika komanso chikondi chokhulupirika zimateteza mfumu.+Mfumuyo ikamasonyeza chikondi chokhulupirika, mpando wake wachifumu umakhazikika.+ Miyambo 29:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Mfumu ikamaweruza anthu osauka mwachilungamo,+Idzapitiriza kulamulira mpaka kalekale.+
44 Kenako mfumuyo inauza Simeyi kuti: “Iweyo ukudziwa mumtima mwako zoipa zonse zimene unachitira Davide bambo anga.+ Yehova akubwezera pamutu pako zoipa zimene unachita.+
46 Ndiyeno mfumuyo inalamula Benaya mwana wa Yehoyada kuti aphe Simeyi ndipo anamuphadi.+ Choncho ufumu unakhazikika mʼmanja mwa Solomo.+
28 Kukhulupirika komanso chikondi chokhulupirika zimateteza mfumu.+Mfumuyo ikamasonyeza chikondi chokhulupirika, mpando wake wachifumu umakhazikika.+