-
2 Mafumu 17:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Yehova ankachenjeza Aisiraeli ndi Ayuda kudzera mwa aneneri ake onse ndiponso amasomphenya onse+ kuti: “Siyani njira zanu zoipa+ ndipo muzisunga malamulo anga, mogwirizana ndi malamulo onse amene ndinalamula makolo anu ndiponso amene ndinakutumizirani kudzera mwa atumiki anga, aneneri.” 14 Koma iwo sanamvere ndipo anali ankhutukumve* ngati makolo awo amene sanasonyeze chikhulupiriro mwa Yehova Mulungu wawo.+
-