-
Yeremiya 38:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Ndiyeno Yeremiya anauza Zedekiya kuti: “Yehova, Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Mukadzipereka mʼmanja mwa akalonga* a mfumu ya Babulo, mudzakhalabe ndi moyo ndipo mzindawu sudzawotchedwa ndi moto komanso inuyo ndi banja lanu mudzakhalabe ndi moyo.+ 18 Koma ngati simudzadzipereka mʼmanja mwa akalonga* a mfumu ya Babulo, mzindawu udzaperekedwa mʼmanja mwa Akasidi ndipo adzauwotcha ndi moto.+ Inuyo simudzathawa mʼmanja mwawo.’”+
-