4 Mʼchaka cha 9 cha ufumu wa Zedekiya, mʼmwezi wa 10, pa tsiku la 10 la mweziwo, Nebukadinezara mfumu ya Babulo anabwera ku Yerusalemu pamodzi ndi asilikali ake onse. Anabwera kudzamenyana ndi anthu amumzindawo ndipo anamanga msasa komanso mpanda kuzungulira mzinda wonsewo.+