-
2 Mafumu 25:18-21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anatenganso Seraya+ wansembe wamkulu, Zefaniya+ wansembe wachiwiri ndi alonda atatu apakhomo.+ 19 Mumzindawo anatengamonso nduna imodzi yapanyumba ya mfumu imene inkayangʼanira asilikali. Anatenganso anzake 5 a mfumu amene anawapeza mumzindawo. Komanso anatenga mlembi wa mkulu wa asilikali yemwe ankasonkhanitsa anthu ndiponso amuna 60 mwa anthu wamba amene anawapeza mumzindawo. 20 Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu anatenga anthuwa nʼkupita nawo ku Ribila kwa mfumu ya Babulo.+ 21 Mfumu ya Babuloyo inapha anthuwo ku Ribila mʼdziko la Hamati.+ Choncho Ayuda anatengedwa kudziko lawo nʼkupita nawo ku ukapolo.+
-