-
Yeremiya 37:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Kenako Mfumu Zedekiya inatuma anthu kuti akatenge Yeremiya.+ Atabwera naye, mfumuyo inamufunsa mafunso mwachinsinsi mʼnyumba mwake. Mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi pali mawu aliwonse ochokera kwa Yehova?” Yeremiya anayankha kuti: “Eya alipo!” Ndipo anapitiriza kuti: “Inuyo mudzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya Babulo!”+
-
-
Yeremiya 39:5-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Koma asilikali a Akasidi anawathamangitsa ndipo Zedekiya anamupeza mʼchipululu cha Yeriko.+ Anamugwira nʼkupita naye kwa Mfumu Nebukadinezara* ya Babulo ku Ribila,+ mʼdziko la Hamati,+ kumene Nebukadinezara anamuweruza. 6 Zitatero mfumu ya Babulo inapha ana aamuna a Zedekiya ku Ribila, Zedekiyayo akuona. Inaphanso anthu onse olemekezeka a ku Yuda.+ 7 Mfumu ya Babulo inachititsa khungu maso a Zedekiya ndipo kenako inamumanga mʼmaunyolo akopa* kuti apite naye ku Babulo.+
-
-
Yeremiya 52:9-11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Kenako Akasidiwo anagwira mfumuyo nʼkupita nayo ku Ribila kwa mfumu ya Babulo mʼdziko la Hamati ndipo anaipatsa chigamulo. 10 Ndipo mfumu ya Babulo inapha ana aamuna a Zedekiya, iye akuona. Inaphanso akalonga onse a ku Yuda ku Ribila komweko. 11 Kenako mfumu ya Babulo inachititsa khungu Zedekiya,+ inamumanga ndi maunyolo akopa* nʼkupita naye ku Babulo ndipo inamuika mʼndende mpaka tsiku la imfa yake.
-