-
Yeremiya 21:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Yeremiya analandira mawu ochokera kwa Yehova pamene Mfumu Zedekiya+ inatumiza Pasuri+ mwana wa Malikiya ndi Zefaniya+ mwana wa Maaseya, wansembe, kuti akamupemphe kuti: 2 “Chonde tifunsire kwa Yehova chifukwa Nebukadinezara,* mfumu ya ku Babulo, akufuna kuchita nafe nkhondo.+ Mwina Yehova atichitira imodzi mwa ntchito zake zodabwitsa moti Nebukadinezarayo atichokera.”+
-