-
Ezekieli 38:4-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Ine ndidzakubweza nʼkukukola chibwano ndi ngowe.+ Kenako ndidzakupititsa kunkhondo limodzi ndi asilikali ako onse,+ mahatchi ako ndi amuna okwera pamahatchi ndipo onsewo adzavala mwaulemerero. Iwo adzakhala gulu lalikulu lonyamula zishango zazikulu ndi zazingʼono, ndipo onsewo ndi aluso lomenya nkhondo pogwiritsa ntchito malupanga. 5 Udzabwera limodzi ndi asilikali a ku Perisiya, Itiyopiya ndi Puti.+ Onsewa adzanyamula zishango zazingʼono ndipo adzavala zipewa. 6 Udzabweranso ndi Gomeri ndi magulu ake onse a asilikali, komanso ana a Togarima+ ochokera kumadera akutali kwambiri akumpoto. Iwo adzabwera ndi magulu awo onse a asilikali. Choncho iwe udzabwera ndi mitundu yambiri ya anthu.+
-
-
Chivumbulutso 19:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Ndinaonanso mngelo ataimirira padzuwa. Iye anafuula ndi mawu okweza kwa mbalame zonse zouluka chapafupi mumlengalenga kuti: “Bwerani kuno, dzasonkhaneni kuphwando lalikulu la Mulungu la chakudya chamadzulo,+ 18 kuti mudzadye minofu ya mafumu, ya akuluakulu a asilikali, ya amuna amphamvu,+ ya mahatchi ndi ya amene akwera pamahatchiwo,+ minofu ya onse, ya mfulu ndi ya akapolo, ya olemekezeka ndi ya onyozeka.”
-