-
Nehemiya 10:35-37Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
35 Tinalonjezanso kuti chaka chilichonse tizibweretsa kunyumba ya Yehova zipatso zoyambirira kupsa zamʼdziko lathu komanso za mtengo uliwonse.+ 36 Tizibweretsanso ana athu aamuna oyamba kubadwa ndiponso a ziweto zathu+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo. Tizibweretsa ana oyamba kubadwa a ngʼombe ndi nkhosa zathu. Tizibweretsa zimenezi kunyumba ya Mulungu wathu, kwa ansembe amene amatumikira mʼnyumba ya Mulungu wathu.+ 37 Komanso tizibweretsa ufa woyambirira wamisere,+ zopereka zathu, zipatso za mtengo uliwonse,+ vinyo watsopano ndi mafuta+ kwa ansembe mʼzipinda zosungira katundu* mʼnyumba ya Mulungu wathu.+ Tifunikanso kubweretsa chakhumi kwa Alevi pa zinthu zochokera mʼdziko lathu+ chifukwa Aleviwo ndi amene amatolera chakhumi kuchokera mʼmizinda yathu yonse ya zaulimi.
-