28 Onse ndi anthu ouma khosi kwambiri,+
Amayenda uku ndi uku nʼkumanena miseche.+
Iwo ali ngati kopa ndi chitsulo,
Onsewo ndi anthu achinyengo.
29 Zipangizo zopemerera moto zapsa ndi moto.
Ndipo pamotopo patuluka mtovu.
Munthu wakhala akuyenga chitsulo mobwerezabwereza koma osaphula kanthu,+
Ndipo zoipa sizinachotsedwemo.+
30 Ndithu, anthu adzawatchula kuti siliva wokanidwa,
Chifukwa Yehova wawakana.”+