-
Yesaya 46:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Pali anthu amene amakhuthula golide mʼzikwama zawo.
Amayeza siliva pasikelo.
Iwo amalemba ganyu mmisiri wa zitsulo ndipo amapanga mulungu ndi zinthu zimenezi.+
Kenako anthuwo amayamba kumuweramira ndi kumulambira.*+
7 Iwo amamunyamula pamapewa awo.+
Amamutenga nʼkukamuika pamalo ake ndipo mulunguyo amangoima pomwepo.
Sasuntha pamene amuikapo.+
Anthuwo amamuitana mofuula, koma sayankha.
Sangapulumutse munthu amene ali pamavuto.+
-