7 Ndifotokoza zimene Yehova wanena.
Iye wandiuza kuti: “Iwe ndiwe mwana wanga,+
Lero, ine ndakhala bambo ako.+
8 Tandipempha, ndipo ndikupatsa mitundu ya anthu kuti ikhale cholowa chako,
Ndiponso dziko lonse lapansi kuti likhale lako.+
9 Mitunduyo udzaiphwanya ndi ndodo yachifumu yachitsulo,+
Ndipo udzaiswa ngati chiwiya chadothi.”+