-
Yesaya 9:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
Iye adzapatsidwa dzina lakuti Mlangizi Wodabwitsa,+ Mulungu Wamphamvu,+ Atate Wamuyaya, Kalonga Wamtendere.
7 Ulamuliro* wake udzafika kutali
Ndipo mtendere sudzatha,+
Pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso mu ufumu wake
Kuti iye achititse ufumuwo kukhazikika+ ndiponso kukhala wolimba
Pogwiritsa ntchito chilungamo+ ndiponso mtima wowongoka,+
Kuyambira panopa mpaka kalekale.
Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.
-
-
Yesaya 16:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Kenako mpando wachifumu udzakhazikika chifukwa cha chikondi chokhulupirika.
-
-
Ezekieli 37:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yawo+ ndipo onsewo adzakhala ndi mʼbusa mmodzi.+ Iwo adzayenda motsatira zigamulo zanga ndiponso kusunga malamulo anga mosamala kwambiri.+ 25 Anthu amenewa adzakhala mʼdziko limene ndinapatsa mtumiki wanga Yakobo, dziko limene makolo anu ankakhala.+ Iwo adzakhala mʼdzikomo ndi ana awo* komanso zidzukulu zawo+ mpaka kalekale.+ Davide mtumiki wanga adzakhala mtsogoleri* wawo mpaka kalekale.+
-
-
Luka 1:31-33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Tsopano mvetsera! Udzakhala woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna+ ndipo udzamupatse dzina lakuti Yesu.+ 32 Ameneyu adzakhala wamkulu+ ndipo adzatchedwa Mwana wa Wamʼmwambamwamba.+ Yehova* Mulungu adzamupatsa mpando wachifumu wa Davide atate wake.+ 33 Iye adzalamulira monga Mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya ndipo Ufumu wake sudzatha.”+
-