Yesaya 11:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Nthambi+ idzaphuka pachitsa cha Jese,+Ndipo mphukira+ yotuluka pamizu yake idzabereka zipatso. Yesaya 53:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Iye adzaphuka ngati nthambi+ pamaso pawinawake* ndiponso ngati muzu wotuluka mʼnthaka youma. Saoneka ngati munthu wapadera kapena waulemerero,+Ndipo tikamuona, maonekedwe ake si ochititsa chidwi moti ife nʼkukopeka naye.* Yeremiya 33:15, 16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 ‘Mʼmasiku amenewo ndiponso nthawi imeneyo ndidzameretsera Davide mphukira+ yolungama* ndipo mphukirayo idzaweruza mwachilungamo mʼdzikoli.+ 16 Mʼmasiku amenewo Yuda adzapulumutsidwa+ ndipo Yerusalemu adzakhala mwamtendere.+ Yerusalemu azidzatchulidwa kuti, Yehova Ndi Chilungamo Chathu.’”+ Zekariya 3:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 ‘Tamvetsera iwe Yoswa mkulu wa ansembe ndi anzako amene akhala pansi kutsogolo kwako, chifukwa amuna amenewa ali ngati chizindikiro. Ine ndibweretsa mtumiki wanga+ dzina lake Mphukira.+ Mateyu 2:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Atafika kumeneko anakakhala mumzinda wotchedwa Nazareti+ kuti akwaniritse mawu amene Mulungu ananena kudzera mwa aneneri kuti: “Iye adzatchedwa Mnazareti.”*+
2 Iye adzaphuka ngati nthambi+ pamaso pawinawake* ndiponso ngati muzu wotuluka mʼnthaka youma. Saoneka ngati munthu wapadera kapena waulemerero,+Ndipo tikamuona, maonekedwe ake si ochititsa chidwi moti ife nʼkukopeka naye.*
15 ‘Mʼmasiku amenewo ndiponso nthawi imeneyo ndidzameretsera Davide mphukira+ yolungama* ndipo mphukirayo idzaweruza mwachilungamo mʼdzikoli.+ 16 Mʼmasiku amenewo Yuda adzapulumutsidwa+ ndipo Yerusalemu adzakhala mwamtendere.+ Yerusalemu azidzatchulidwa kuti, Yehova Ndi Chilungamo Chathu.’”+
8 ‘Tamvetsera iwe Yoswa mkulu wa ansembe ndi anzako amene akhala pansi kutsogolo kwako, chifukwa amuna amenewa ali ngati chizindikiro. Ine ndibweretsa mtumiki wanga+ dzina lake Mphukira.+
23 Atafika kumeneko anakakhala mumzinda wotchedwa Nazareti+ kuti akwaniritse mawu amene Mulungu ananena kudzera mwa aneneri kuti: “Iye adzatchedwa Mnazareti.”*+