-
2 Mafumu 21:18-20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Kenako Manase, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda mʼmunda wapanyumba pake, mʼmunda wa Uziza.+ Ndiyeno mwana wake Amoni anakhala mfumu mʼmalo mwake.
19 Amoni+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 22 ndipo analamulira zaka ziwiri ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Yotiba ndipo dzina lawo linali Mesulemeti mwana wa Haruzi. 20 Amoni ankachita zoipa pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira Manase bambo ake.+
-