-
Maliko 9:2-8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Patapita masiku 6, Yesu anatenga Petulo, Yakobo ndi Yohane nʼkukwera nawo mʼphiri lalitali kwaokhaokha. Ndiyeno iye anasintha maonekedwe ake iwo akuona.+ 3 Malaya ake akunja anayamba kunyezimira nʼkuyera kwambiri kuposa mmene wochapa zovala aliyense padziko lapansi angayeretsere zovala. 4 Komanso Eliya ndi Mose anaonekera kwa iwo ndipo ankakambirana ndi Yesu. 5 Ndiye Petulo anauza Yesu kuti: “Rabi, zingakhale bwino ife titamakhala pano. Choncho timange matenti atatu pano, imodzi yanu, imodzi ya Mose ndi ina ya Eliya.” 6 Petulo sanadziwe choti anene, chifukwa ophunzirawo anachita mantha kwambiri. 7 Ndiyeno kunachita mtambo umene unawaphimba. Kenako panamveka mawu+ kuchokera mumtambomo akuti: “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa.+ Muzimumvera.”+ 8 Kenako iwo anayangʼana uku ndi uku ndipo anangoona kuti palibe wina aliyense koma Yesu yekha basi.
-
-
Luka 9:28-36Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Patapita masiku pafupifupi 8 atanena mawu amenewa, iye anatenga Petulo, Yohane ndi Yakobo nʼkukwera nawo phiri kukapemphera.+ 29 Pamene ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake anasintha ndipo chovala chake chinaoneka choyera kwambiri ndi chonyezimira. 30 Ndiyeno panaoneka anthu awiri akukambirana naye. Anthu amenewa anali Mose ndi Eliya. 31 Iwo anaonekera ndi ulemerero ndipo anayamba kukambirana za mmene Yesu adzachokere mʼdzikoli, ku Yerusalemu.+ 32 Apa nʼkuti Petulo ndi ena amene anali naye atatheratu ndi tulo. Koma tulo titawathera, anaona ulemerero wake+ ndiponso amuna awiri ataima naye. 33 Ndiyeno pamene amunawa ankasiyana naye, Petulo anauza Yesu kuti: “Mlangizi, zingakhale bwino ife titamakhala pano. Choncho timange matenti atatu pano, imodzi yanu, imodzi ya Mose ndi ina ya Eliya.” Koma iye sankazindikira zimene ankanena. 34 Pamene ankanena zimenezi, kunachita mtambo ndipo unayamba kuwaphimba. Mtambowo utawaphimba, anachita mantha. 35 Ndiyeno panamveka mawu+ kuchokera mumtambomo akuti: “Uyu ndi Mwana wanga, amene ndinamusankha.+ Muzimumvera.”+ 36 Pamene mawuwo ankamveka, anaona kuti Yesu ali yekha. Koma iwo anakhala chete ndipo sanauze aliyense mʼmasiku amenewo chilichonse pa zimene anaonazo.+
-