Levitiko 19:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Usabwezere choipa+ kapena kusungira chakukhosi anthu a mtundu wako. Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.+ Ine ndine Yehova. Maliko 12:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Lachiwiri ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’+ Palibe lamulo lina lalikulu kuposa amenewa.” Luka 10:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Iye anayankha kuti: “‘Muzikonda Yehova* Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, mphamvu zanu zonse ndi maganizo anu onse.’+ Komanso ‘uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’”+ Akolose 3:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Koma kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi,+ chifukwa chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.+ Yakobo 2:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Ndiye ngati mukutsatira lamulo lachifumu lakuti, “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha,”+ ngati mmene lemba limanenera, mukuchita bwino ndithu. 1 Petulo 1:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Popeza mwadziyeretsa pokhala omvera choonadi cha mʼMawu a Mulungu ndipo tsopano mumakonda abale mopanda chinyengo,+ muzikondana kwambiri kuchokera mumtima.+
18 Usabwezere choipa+ kapena kusungira chakukhosi anthu a mtundu wako. Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.+ Ine ndine Yehova.
31 Lachiwiri ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’+ Palibe lamulo lina lalikulu kuposa amenewa.”
27 Iye anayankha kuti: “‘Muzikonda Yehova* Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, mphamvu zanu zonse ndi maganizo anu onse.’+ Komanso ‘uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’”+
14 Koma kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi,+ chifukwa chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.+
8 Ndiye ngati mukutsatira lamulo lachifumu lakuti, “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha,”+ ngati mmene lemba limanenera, mukuchita bwino ndithu.
22 Popeza mwadziyeretsa pokhala omvera choonadi cha mʼMawu a Mulungu ndipo tsopano mumakonda abale mopanda chinyengo,+ muzikondana kwambiri kuchokera mumtima.+