-
2 Mbiri 24:20-22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, Zekariya mwana wa wansembe Yehoyada+ anaimirira pamalo okwera nʼkuyamba kuuza anthuwo kuti: “Mulungu woona wanena kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mukuphwanya malamulo a Yehova? Zinthutu sizikukuyenderani bwino. Poti mwamusiya Yehova, iyenso akusiyani.’”+ 21 Koma anthuwo anamʼkonzera chiwembu+ ndipo anamʼponya miyala pabwalo la nyumba ya Yehova, atalamulidwa ndi mfumu.+ 22 Choncho Mfumu Yehoasi sanakumbukire chikondi chokhulupirika chimene Yehoyada bambo a Zekariya anamusonyeza ndipo anapha mwana wawo, yemwe pakufa ananena kuti: “Yehova aone zimene mwachitazi nʼkukubwezerani.”+
-