-
Maliko 13:21-23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Komanso pa nthawiyo, munthu akadzakuuzani kuti, ‘Onani! Khristu uja ali kuno,’ kapena, ‘Onani! Ali uko,’ musadzakhulupirire zimenezo.+ 22 Chifukwa kudzabwera anthu onamizira kuti ndi Khristu ndiponso aneneri abodza+ ndipo adzachita zizindikiro komanso zodabwitsa kuti ngati nʼkotheka, adzasocheretse osankhidwawo. 23 Choncho inuyo musamale.+ Ine ndakuuziranitu zinthu zonse.
-