-
Luka 8:35-37Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
35 Kenako anthu anapita kukaona zomwe zinachitikazo. Iwo atafika kwa Yesu anapeza munthu amene anamutulutsa ziwanda uja atakhala pansi pafupi ndi Yesu. Munthuyo anali atavala bwino komanso maganizo ake ali bwinobwino ndipo iwo anachita mantha. 36 Amene anaona zimene zinachitikazo anawafotokozera mmene munthu wogwidwa ziwandayo anamuchiritsira. 37 Kenako gulu lonse lochokera mʼmidzi yapafupi ya Agerasa linamupempha kuti achoke kwawoko, chifukwa linagwidwa ndi mantha aakulu. Zitatero iye anakwera ngalawa kuti azipita.
-