-
Maliko 1:29-31Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Zitatero iwo anachoka kusunagogeko nʼkupita kunyumba kwa Simoni ndi Andireya. Yakobo ndi Yohane nawonso anapita nawo.+ 30 Koma apongozi aakazi a Simoni+ anali chigonere, akudwala malungo.* Mwamsanga iwo anamuuza za mayiwo. 31 Choncho iye anapita kumene kunali mayiwo ndipo anawagwira dzanja nʼkuwadzutsa. Atatero malungowo anatheratu moti mayiwo anayamba kuwatumikira.
-