Ezekieli 34:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 “Nkhosa imene yasowa ndidzaifunafuna,+ imene yasochera ndidzaibweza. Imene yavulala ndidzaimanga povulalapo ndipo imene ili yofooka ndidzailimbitsa, koma yonenepa ndi yamphamvu ndidzaiwononga. Ndidzaipatsa chiweruzo kuti chikhale chakudya chake.” Mateyu 9:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Choncho pitani mukaphunzire tanthauzo la mawu akuti: ‘Ndikufuna chifundo, osati nsembe.’+ Chifukwa ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.” Mateyu 15:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Iye anayankha kuti: “Ine sananditumize kwa wina aliyense koma kwa nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.”+ Luka 15:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 “Ndi ndani pakati panu amene atakhala ndi nkhosa 100, imodzi nʼkusowa, sangasiye nkhosa 99 zinazo mʼchipululu nʼkupita kukafunafuna imodzi imene yasowayo mpaka ataipeza?+ Aroma 5:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Koma Mulungu akutisonyeza chikondi chake, chifukwa pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.+ 1 Timoteyo 1:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Mawu akuti Khristu Yesu anabwera mʼdziko kudzapulumutsa ochimwa,+ ndi mawu oona komanso oyenera kuwavomereza ndi mtima wonse. Pa ochimwa amenewa, ine ndiye wochimwa kwambiri.+
16 “Nkhosa imene yasowa ndidzaifunafuna,+ imene yasochera ndidzaibweza. Imene yavulala ndidzaimanga povulalapo ndipo imene ili yofooka ndidzailimbitsa, koma yonenepa ndi yamphamvu ndidzaiwononga. Ndidzaipatsa chiweruzo kuti chikhale chakudya chake.”
13 Choncho pitani mukaphunzire tanthauzo la mawu akuti: ‘Ndikufuna chifundo, osati nsembe.’+ Chifukwa ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.”
24 Iye anayankha kuti: “Ine sananditumize kwa wina aliyense koma kwa nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.”+
4 “Ndi ndani pakati panu amene atakhala ndi nkhosa 100, imodzi nʼkusowa, sangasiye nkhosa 99 zinazo mʼchipululu nʼkupita kukafunafuna imodzi imene yasowayo mpaka ataipeza?+
15 Mawu akuti Khristu Yesu anabwera mʼdziko kudzapulumutsa ochimwa,+ ndi mawu oona komanso oyenera kuwavomereza ndi mtima wonse. Pa ochimwa amenewa, ine ndiye wochimwa kwambiri.+