-
Mateyu 27:57-60Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
57 Tsopano madzulo kwambiri, kunabwera munthu wina wachuma wa ku Arimateya, dzina lake Yosefe, amenenso anakhala wophunzira wa Yesu.+ 58 Iye anapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu+ ndipo Pilato analamula kuti amupatse mtembowo.+ 59 Yosefe anatenga mtembowo nʼkuukulunga munsalu yoyera yabwino kwambiri,+ 60 ndipo anakauika mʼmanda*+ ake atsopano amene anawasema muthanthwe. Kenako atagubuduza chimwala chachikulu nʼkutseka pakhomo la mandawo,* anachoka.
-
-
Maliko 15:43-46Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
43 kunabwera Yosefe wa ku Arimateya, munthu wodziwika wa mʼKhoti Lalikulu la Ayuda, amenenso ankayembekezera Ufumu wa Mulungu. Iye anapita molimba mtima kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu.+ 44 Koma Pilato ankakayikira ngati anali atamwalira kale. Choncho anaitanitsa mtsogoleri wa asilikali nʼkumufunsa ngatidi Yesu anali atamwalira kale. 45 Atatsimikizira kuchokera kwa mtsogoleri wa asilikaliyo, analola kuti Yosefe akatenge mtembowo. 46 Ndiyeno Yosefe atagula nsalu yabwino kwambiri nʼkumutsitsa, anamukulunga ndi nsaluyo nʼkumuika mʼmanda*+ amene anawasema mʼthanthwe. Kenako anagubuduza chimwala nʼkutseka pakhomo la mandawo.+
-