-
Machitidwe 22:6-11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Koma ndili mʼnjira, nditatsala pangʼono kufika ku Damasiko, dzuwa lili pamutu, mwadzidzidzi kunawala kwambiri. Kuwala kumeneku kunali kochokera kumwamba ndipo kunazungulira pamene ine ndinali.+ 7 Ndinagwa pansi ndipo ndinamva mawu akuti: ‘Saulo! Saulo! Nʼchifukwa chiyani ukundizunza?’ 8 Ine ndinayankha kuti, ‘Ndinu ndani Mbuyanga?’ Ndipo anandiuza kuti, ‘Ndine Yesu wa ku Nazareti, amene iwe ukumuzunza.’ 9 Amuna amene ndinali nawo anaona kuwalako, koma sanamvetse mawu amene ankalankhula ndi inewo. 10 Ndiye ine ndinati, ‘Nditani Ambuye?’ Ambuyewo anandiuza kuti, ‘Nyamuka ndipo upite ku Damasiko. Kumeneko ukauzidwa zonse zimene zakonzedwa kuti uchite.’+ 11 Koma popeza sindinkatha kuona chilichonse chifukwa cha ulemerero wa kuwalako, anthu amene ndinali nawo aja, anandigwira dzanja mpaka kukafika ku Damasiko.
-
-
Machitidwe 26:13-18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Koma ndili mʼnjira dzuwa lili pamutu, inu mfumu, ndinaona kuwala kochokera kumwamba koposa kuwala kwa dzuwa ndipo kunandizungulira ineyo ndiponso anthu amene ndinali nawo pa ulendowu.+ 14 Ndiyeno tonse titagwa pansi, ndinamva mawu akundiuza mʼChiheberi kuti, ‘Saulo! Saulo! Nʼchifukwa chiyani ukundizunza? Ukungovutika popitiriza kuchita ngati nyama imene ikuponya miyendo yake nʼkumamenya zisonga zotosera.’* 15 Koma ine ndinati: ‘Ambuye, ndinu ndani kodi?’ Ndipo Ambuye anati: ‘Ndine Yesu amene iwe ukumuzunza. 16 Komabe dzuka ndipo uimirire. Ndaonekera kwa iwe kuti ndikusankhe kuti ukhale mtumiki komanso mboni ya zinthu zonse zokhudza ine, zomwe waona ndiponso zimene ndidzakuonetsa.+ 17 Ndipo ndidzakupulumutsa kwa anthu awa komanso kwa anthu a mitundu ina kumene ndikukutumiza+ 18 kuti ukatsegule maso awo,+ kuwachotsa mumdima+ nʼkuwapititsa kowala+ ndiponso kuwachotsa mʼmanja mwa Satana+ nʼkuwapititsa kwa Mulungu. Ukachite zimenezi kuti machimo awo akhululukidwe+ nʼkulandira cholowa pamodzi ndi oyeretsedwa chifukwa chondikhulupirira.’
-