11 Choncho anthu inu munayandikira nʼkuimirira mʼmunsi mwa phiri. Phirilo linkayaka moto umene unkafika kumwamba, ndipo kunali mdima ndi mtambo wakuda.+ 12 Ndiyeno Yehova anayamba kukulankhulani kuchokera mʼmoto.+ Inu munamva mawu koma simunaone kalikonse.+ Munangomva mawu okha basi.+