12 Kodi ndi ndani pakati panu amene amakonda moyo,
Ndipo angakonde atakhala ndi moyo wabwino kwa masiku ambiri?+
נ [Nun]
13 Ndiyetu muteteze lilime lanu ku zinthu zoipa,+
Komanso milomo yanu kuti isalankhule chinyengo.+
ס [Samekh]
14 Siyani kuchita zinthu zoipa ndipo muzichita zabwino.+
Yesetsani kukhala mwamtendere ndi ena komanso kuulimbikitsa.+
ע [Ayin]
15 Maso a Yehova ali pa olungama,+
Ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.+
פ [Pe]
16 Koma Yehova amakwiyira anthu ochita zoipa,
Iye adzawawononga ndipo sadzakumbukiridwanso padziko lapansi.+