-
Chivumbulutso 12:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Ndinamva mawu ofuula kumwamba akuti:
“Tsopano chipulumutso,+ mphamvu, Ufumu wa Mulungu wathu+ ndi ulamuliro wa Khristu wake zafika, chifukwa woneneza abale athu waponyedwa pansi. Iye amawaneneza masana ndi usiku pamaso pa Mulungu wathu.+ 11 Iwo anamugonjetsa+ chifukwa cha magazi a Mwanawankhosa+ ndiponso chifukwa cha uthenga umene ankalalikira+ ndipo anali okonzeka kufa.+
-