Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la ana a Kora.+ Mogwirizana ndi kaimbidwe ka Alamoti.* Nyimbo.
46 Mulungu ndi pothawira pathu komanso mphamvu yathu,+
Thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya mavuto.+
2 Nʼchifukwa chake sitidzaopa, ngakhale dziko lapansi litasintha,
Ndiponso ngakhale mapiri atagwera mʼnyanja yakuya nʼkumira,+
3 Ngakhale madzi amʼnyanjayo atawinduka nʼkuchita thovu,+
Ndiponso ngakhale mapiri atagwedezeka chifukwa cha kuwinduka kwa nyanjayo. (Selah)
4 Pali mtsinje umene nthambi zake zimachititsa kuti anthu amumzinda wa Mulungu asangalale,+
Chihema chachikulu chopatulika cha Wamʼmwambamwamba.
5 Mulungu ali mumzindawo+ ndipo sungagonjetsedwe.
Mulungu adzauthandiza mʼbandakucha.+
6 Mitundu ya anthu inachita phokoso, maufumu anagonjetsedwa.
Iye analankhula mokweza mawu ndipo dziko lapansi linasungunuka.+
7 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ali ndi ife.+
Mulungu wa Yakobo ndi malo athu othawirako otetezeka.* (Selah)
8 Bwerani mudzaone ntchito za Yehova,
Mmene wachitira zinthu zodabwitsa padziko lapansi.
9 Akuthetsa nkhondo padziko lonse lapansi.+
Wathyola uta ndi kupindapinda mkondo.
Ndipo wawotcha pamoto magaleta ankhondo.*
10 “Gonjerani ndipo mudziwe kuti ine ndine Mulungu.