Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la ana a Kora+ mogwirizana ndi kaimbidwe ka Atsikana.
46 Mulungu ndiye pothawira pathu ndi mphamvu yathu,+
Thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya masautso.+
2 N’chifukwa chake sitidzaopa, ngakhale dziko lapansi litasintha,+
Ndiponso ngakhale mapiri atagwedezeka ndi kumira m’nyanja yaikulu.+
3 Ngakhale madzi a m’nyanjayo atawinduka ndi kuchita thovu,+
Ndiponso ngakhale mapiri atagwedezeka chifukwa cha phokoso la nyanja yaikuluyo.+ [Seʹlah.]
4 Pali mtsinje womwe nthambi zake zimachititsa anthu a mumzinda wa Mulungu kukondwera,+
Chihema chachikulu chopatulika koposa cha Wam’mwambamwamba.+
6 Mitundu ya anthu inachita phokoso,+ maufumu anagwedezeka.
Iye anatulutsa mawu ndipo dziko lapansi linasungunuka.+
7 Yehova wa makamu ali ndi ife.+
Mulungu wa Yakobo ndiye malo athu okwezeka ndiponso achitetezo.+ [Seʹlah.]
8 Bwerani anthu inu, onani ntchito za Yehova,+
Onani mmene wakhazikitsira zinthu zodabwitsa padziko lapansi.+
9 Akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+
Wathyola uta ndi kuduladula mkondo.+
Ndipo watentha magaleta pamoto.+