Ekisodo
27 “Upange guwa lansembe lamatabwa a mthethe,+ mulitali likhale mamita awiri,* ndipo mulifupi likhalenso mamita awiri. Guwalo likhale lofanana muyezo wake mbali zake zonse 4, ndipo kutalika kwake kuchokera pansi mpaka mʼmwamba likhale masentimita 134.+ 2 Upange nyanga mʼmakona ake+ 4. Nyangazo zituluke mʼmakonawo ndipo ulikute ndi kopa.*+ 3 Kenako upange ndowa zake zochotsera phulusa,* mafosholo ake, mbale zake zolowa, mafoloko aakulu ndi zopalira moto zake. Ziwiya zake zonse uzipange ndi kopa.+ 4 Upangenso sefa wa zitsulo zakopa zolukanalukana, ndipo pasefayo upangepo mphete 4 zakopa mʼmakona ake 4. 5 Ulowetse sefayo chapakati pa guwa lansembe, mʼmunsi mwa mkombero. 6 Guwalo ulipangire ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe ndipo uzikute ndi kopa. 7 Ndodo zonyamulirazo uzizilowetsa mumphetezo mʼmbali zonse ziwiri za guwalo polinyamula.+ 8 Upange bokosi lamatabwa losatseka pansi. Lipangidwe mogwirizana ndi mmene ndakusonyezera mʼphiri.+
9 Ndiyeno upange bwalo+ la chihema. Kumbali yakumʼmwera, bwalolo ulitchinge ndi mpanda wa nsalu za ulusi wopota wabwino kwambiri. Mpandawo ukhale mamita 45 mulitali mwake kumbali imodziyo.+ 10 Upangenso zipilala zake 20 ndi zitsulo 20 zakopa zokhazikapo zipilalazo. Tizitsulo ta zipilala tokolowekapo nsalu ndi tolumikizira take tikhale tasiliva. 11 Nsalu yambali yakumpoto kwa mpandawo ikhalenso mamita 45 mulitali mwake, ndipo kukhale zipilala 20 ndi zitsulo 20 zakopa zokhazikapo zipilalazo. Tizitsulo tokolowekapo nsalu ndi tolumikizira take tikhale tasiliva. 12 Mulifupi mwa bwalolo, kumbali yakumadzulo, mpanda wa nsaluwo kutalika kwake ukhale mamita 23, ndipo ukhale ndi zipilala 10 ndi zitsulo 10 zokhazikapo zipilalazo. 13 Ndipo mulifupi mwa bwalolo kumbali yakumʼmawa, kotulukira dzuwa, kukhale mamita 23. 14 Kudzanja lamanja la geti la bwalolo, mpanda wa nsaluwo ukhale mamita 7 kutalika kwake. Kukhale zipilala zitatu ndi zitsulo zitatu zokhazikapo zipilalazo.+ 15 Ndipo kudzanja lamanzere la geti la bwalolo mpanda wa nsaluwo ukhale mamita 7. Kukhale zipilala zitatu ndi zitsulo zitatu zokhazikapo zipilalazo.
16 Pakhomo la bwalolo pakhale nsalu yowomba yokwana mamita 9 mulitali mwake. Ikhale ya ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+ Pakhale zipilala 4 ndi zitsulo 4 zokhazikapo zipilalazo.+ 17 Zipilala zonse kuzungulira bwalo lonselo zikhale ndi tolumikizira tasiliva, ndipo tizitsulo tokolowekapo nsalu tikhalenso tasiliva, koma zitsulo zokhazikapo zipilalazo zikhale zakopa.+ 18 Bwalolo mulitali mwake likhale mamita 45,+ mulifupi mwake mamita 23, ndipo kutalika kwake kuchoka pansi mpaka mʼmwamba kukhale mamita atatu. Nsalu zake zikhale za ulusi wopota wabwino kwambiri, ndipo zitsulo zake zokhazikapo zipilala zikhale zakopa. 19 Ziwiya zonse zogwiritsa ntchito pa utumiki wonse wapachihema, zikhomo zake zonse ndi zikhomo zonse za nsalu yampanda wa bwalolo zikhale zakopa.+
20 Ulamule Aisiraeli kuti akupezere mafuta ounikira oyenga bwino kwambiri a maolivi, kuti nyale ziziyaka nthawi zonse.+ 21 Mʼchihema chokumanako,* kunja kwa katani imene ili pafupi ndi Umboni,+ Aroni ndi ana ake azionetsetsa kuti nyale zikuyaka pamaso pa Yehova, kuyambira madzulo mpaka mʼmawa.+ Limeneli ndi lamulo kwa Aisiraeli kuti mibadwo yawo izichita zimenezi mpaka kalekale.”+