Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
126 Yehova atabwezeretsa anthu a ku Ziyoni kuchokera ku ukapolo,+
Tinkangoona ngati tikulota.
2 Pa nthawiyo tinaseka
Ndipo tinasangalala kwambiri.+
Pa nthawi imeneyo anthu a mitundu ina anayamba kuuzana kuti:
“Yehova wachitira anthu amenewa zinthu zazikulu.”+
3 Yehova watichitira zazikulu,+
Ndipo tasangalala kwambiri.
4 Inu Yehova, bwezeretsani anthu athu amene anagwidwa ukapolo,
Ngati mmene mvula imadzazitsira mitsinje ya ku Negebu.
5 Amene akukhetsa misozi pofesa mbewu
Adzakolola akufuula mosangalala.
6 Amene akupitabe kumunda, ngakhale kuti akulira,
Atasenza thumba lake la mbewu,
Ndithu adzabwerako akufuula mosangalala,+
Atasenza mtolo wake wa zokolola.+