Ekisodo
9 Choncho Yehova anauza Mose kuti: “Pita kwa Farao, ukamuuze kuti, ‘Yehova Mulungu wa Aheberi wanena kuti: “Lola anthu anga apite kuti akanditumikire.+ 2 Koma ukakana kuti apite nʼkuwaumirirabe, 3 dziwa kuti dzanja la Yehova+ lipha ziweto zanu zonse. Mliri waukulu kwambiri+ ugwera mahatchi,* abulu, ngamila, ngʼombe ndi nkhosa. 4 Ndipo Yehova adzaika malire pakati pa ziweto za Isiraeli ndi ziweto za Iguputo, moti palibe chiweto cha Aisiraeli chimene chidzafe.”’”+ 5 Komanso, Yehova anatchuliratu nthawi kuti: “Mawa, Yehova adzachita zimenezi mʼdzikoli.”
6 Yehova anachitadi zimenezi tsiku lotsatira, moti ziweto zamitundu yonse za Aiguputo zinayamba kufa,+ koma palibe chiweto ngakhale chimodzi cha Aisiraeli chimene chinafa. 7 Ndiye Farao atafufuza anapeza kuti palibe chiweto ngakhale chimodzi cha Aisiraeli chimene chinafa. Ngakhale zinali choncho, Farao anapitiriza kuumitsa mtima wake ndipo sanalole kuti Aisiraeli apite.+
8 Kenako Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: “Tengani phulusa* la mu uvuni lodzaza manja anu awiri ndipo Mose aliponye mʼmwamba Farao akuona. 9 Ndipo lidzachuluka nʼkugwa ngati fumbi padziko lonse la Iguputo. Likatero lidzayambitsa zithupsa pa anthu ndi nyama zomwe, mʼdziko lonse la Iguputo.”
10 Choncho iwo anatenga phulusa la mu uvuni nʼkuima pamaso pa Farao. Kenako Mose analiponya mʼmwamba ndipo linayambitsa zithupsa zimene zinkaphulika pa anthu ndi nyama. 11 Ansembe ochita zamatsenga aja sanathe kuonekera pamaso pa Mose chifukwa cha zithupsazo, popeza zinatuluka pa ansembewo ndi pa Aiguputo onse.+ 12 Koma Yehova analola Farao kuumitsa mtima wake, ndipo sanamvere Mose ndi Aroni, mogwirizana ndi zimene Yehova anauza Mose.+
13 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Mawa ulawirire mʼmamawa kwambiri kukaonana ndi Farao, ndipo ukamuuze kuti: ‘Yehova Mulungu wa Aheberi wanena kuti: “Lola anthu anga apite kuti akanditumikire. 14 Ukakana, nditumiza miliri yanga yonse pa iwe, pa atumiki ako ndi anthu ako, kuti udziwe kuti palibe wofanana ndi ine padziko lonse lapansi.+ 15 Pofika pano ndikanakhala nditatambasula kale dzanja langa nʼkupha iweyo komanso anthu ako ndi mliri woopsa, ndipo ndikanakufafanizani padziko lapansi. 16 Koma ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga komanso kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.+ 17 Kodi ukudzikuzabe pamaso pa anthu anga, pokana kuwalola kuti achoke? 18 Taona, mawa pa nthawi ngati ino ndigwetsa mvula yamphamvu kwambiri yamatalala, matalala amene sanayambe agwapo mu Iguputo mʼmbiri yonse ya dzikoli mpaka lero. 19 Choncho tumiza atumiki ako kuti asonkhanitse ziweto zako zonse ndi zinthu zako zonse zimene zili kunja nʼkuzilowetsa mʼmalo otetezeka. Munthu aliyense komanso nyama iliyonse imene idzapezeke kunja osati mʼnyumba, idzafa chifukwa matalalawo adzawagwera.”’”
20 Aliyense amene anachita mantha ndi mawu a Yehova pakati pa atumiki a Farao analowetsa mwamsanga ziweto zake ndi antchito ake mʼnyumba. 21 Koma aliyense amene sanamvere mawu a Yehova anasiya atumiki ake ndi ziweto zake kunja.
22 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula dzanja lako nʼkuloza kumwamba kuti matalala agwe mʼdziko lonse la Iguputo,+ kuti agwere anthu, nyama ndi zomera zonse mʼdziko la Iguputo.”+ 23 Ndiyeno Mose anatambasula dzanja lake nʼkuloza kumwamba ndi ndodo yake. Atatero, Yehova anachititsa mabingu ndipo anagwetsa matalala ndi moto* padziko lapansi. Choncho Yehova anapitiriza kugwetsa matalala mʼdziko la Iguputo. 24 Ndipo kunagwa matalala komanso moto unkangʼanima. Kunagwa matalala amphamvu kwambiri amene sanaonekepo nʼkale lonse mʼdziko lonse la Iguputo.+ 25 Matalalawo anawononga china chilichonse mʼdziko lonse la Iguputo. Anapha anthu komanso nyama ndipo anawononga zomera zonse zamʼmunda. Anagwetsanso mitengo yonse yamʼdzikolo.+ 26 Koma kudera la Goseni kokha, kumene kunali Aisiraeli, sikunagwe matalala.+
27 Kenako Farao anatumiza atumiki ake kukaitana Mose ndi Aroni nʼkuwauza kuti: “Tsopano ndachimwa. Yehova ndi wolungama, koma ine ndi anthu anga ndife olakwa. 28 Muchonderereni Yehova kuti mabingu ndi matalalawa athe. Mukatero ndikulolani kuti muzipita, ndipo simukhalanso kuno.” 29 Choncho Mose anamuyankha kuti: “Ndikangotuluka mumzinda uno, ndikweza manja anga kwa Yehova. Mabingu asiya ndipo matalala sapitirizanso kugwa kuti mudziwe kuti dziko lapansi ndi la Yehova.+ 30 Koma ndikudziwa kuti ngakhale zimenezi zichitike, inuyo ndi atumiki anu simudzaopa Yehova Mulungu.”
31 Pa nthawi imeneyo mbewu za fulakesi* ndi balere zinawonongeka, chifukwa balere anali atakhwima ndipo fulakesi anali atachita maluwa. 32 Koma tirigu* sanawonongeke, chifukwa amakhwima mochedwa.* 33 Ndiyeno Mose anachoka pamaso pa Farao nʼkutuluka mumzindawo. Kenako anakweza manja ake kwa Yehova, ndipo mabingu ndi matalala zinasiya, mvulanso inasiya kugwa padziko lapansi.+ 34 Farao ataona kuti mvula, matalala ndi mabingu zasiya, anachimwanso ndipo anaumitsa mtima wake,+ iyeyo ndi atumiki ake. 35 Choncho Farao anapitiriza kuumitsa mtima wake ndipo sanalole kuti Aisiraeli apite, mogwirizana ndi zimene Yehova ananena kudzera mwa Mose.+