Danieli
1 Mʼchaka chachitatu cha ufumu wa Mfumu Yehoyakimu+ ya Yuda, Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo inabwera ku Yerusalemu ndipo inazungulira mzindawo.+ 2 Kenako Yehova anapereka Mfumu Yehoyakimu ya Yuda mʼmanja mwake,+ limodzi ndi zina mwa ziwiya za mʼnyumba ya* Mulungu woona. Nebukadinezara anatenga ziwiyazo nʼkupita nazo kudziko la Sinara,*+ kunyumba* ya mulungu wake ndipo anakaziika mʼnyumba yosungiramo chuma ya mulungu wake.+
3 Ndiyeno mfumu inalamula Asipenazi, mkulu wa nduna zapanyumba ya mfumu kuti abweretse ena mwa Aisiraeli,* kuphatikizapo a mʼbanja lachifumu komanso anthu olemekezeka.+ 4 Inalamula kuti abweretse achinyamata* amene analibe chilema chilichonse, ooneka bwino, anzeru, odziwa zinthu, ozindikira+ komanso amene akanatha kutumikira mʼnyumba ya mfumu. Iye ankayenera kuwaphunzitsa chilankhulo komanso zinthu zina zimene Akasidi analemba. 5 Kuwonjezera pamenepo, mfumu inalamula kuti tsiku lililonse aziwapatsa zakudya zabwino za mfumu ndi vinyo wofanana ndi amene mfumu inkamwa. Ankayenera kuwaphunzitsa* kwa zaka zitatu ndipo pambuyo pa zaka zimenezi, ankayenera kuyamba kutumikira mfumu.
6 Pagulu la anyamatawo panali anyamata ena a fuko la Yuda.* Mayina awo anali Danieli,*+ Hananiya,* Misayeli* ndi Azariya.*+ 7 Mkulu wa nduna zapanyumba ya mfumu anapatsa anyamatawa mayina* ena. Danieli anamupatsa dzina lakuti Belitesazara,+ Hananiya anamupatsa dzina lakuti Shadireki,* Misayeli anamupatsa dzina lakuti Misheki* ndipo Azariya anamupatsa dzina lakuti Abedinego.+
8 Koma Danieli anatsimikiza mumtima mwake kuti sadzidetsa ndi zakudya zabwino za mfumu kapena ndi vinyo amene ankamwa. Choncho iye anapempha mkulu wa nduna zapanyumba ya mfumu kuti amulole kuti asadzidetse ndi zinthu zimenezi. 9 Choncho Mulungu woona anachititsa kuti mkulu wa nduna zapanyumba ya mfumu akomere mtima Danieli komanso kumusonyeza chifundo.+ 10 Mkulu wa nduna zapanyumba ya mfumuyo anauza Danieli kuti: “Ine ndikuopa mbuye wanga mfumu, amene walamula kuti muzipatsidwa chakudya ndi zakumwa zimenezi. Ndiye mukuona kuti zitha bwanji akakuonani kuti ndinu owonda kuposa anyamata* ena a msinkhu wanu? Mupangitsa kuti ndikhale* ndi mlandu pamaso pa mfumu.” 11 Koma Danieli anauza munthu amene ankawayangʼanira uja, yemwe mkulu wa nduna zapanyumba ya mfumu anamuika kuti aziyangʼanira Danieli, Hananiya, Misayeli ndi Azariya. Iye anati: 12 “Chonde, mutiyese atumiki anufe kwa masiku 10 ndipo mulole kuti tizipatsidwa zakudya zamasamba ndi madzi akumwa. 13 Kenako mudzayerekeze mmene ifeyo tikuonekera ndi mmene anyamata* amene akudya zakudya zabwino za mfumu akuonekera, ndipo mudzachitire atumiki anufe mogwirizana ndi zimene mudzaone.”
14 Choncho munthu amene ankawayangʼanira uja anavomera kuchita zimene anamupemphazo ndipo anawayesa kwa masiku 10. 15 Masiku 10 amenewo atatha, iwo ankaoneka bwino kwambiri ndipo anali athanzi* kuposa anyamata* onse amene ankadya zakudya zabwino za mfumu. 16 Choncho, amene ankawayangʼanira uja anapitirizabe kuwapatsa zakudya zamasamba mʼmalo mwa zakudya zabwino za mfumu ndi vinyo wake. 17 Mulungu woona anachititsa kuti anyamata* 4 amenewa akhale odziwa zinthu komanso ozindikira zinthu zonse zolembedwa ndipo anawapatsa nzeru. Danieli anamupatsa nzeru zoti azitha kumvetsa bwino masomphenya ndi maloto amtundu uliwonse.+
18 Masiku amene mfumu inanena kuti adzabweretse anyamata aja pamaso pake atakwana,+ mkulu wa nduna zapanyumba ya mfumu uja anabweretsa anyamatawo pamaso pa Nebukadinezara. 19 Mfumuyo italankhula nawo, inaona kuti pagulu lonselo panalibe aliyense amene ankafanana ndi Danieli, Hananiya, Misayeli ndi Azariya.+ Choncho anyamata amenewa anapitiriza kutumikira mfumu. 20 Pa nkhani iliyonse yofunika nzeru komanso kuzindikira, imene mfumu inkawafunsa, inaona kuti iwo anali anzeru kuwirikiza maulendo 10 kuposa ansembe onse ochita zamatsenga ndi anthu onse olankhula ndi mizimu+ amene anali mu ufumu wake wonse. 21 Choncho Danieli anapitiriza kukhala kumeneko mpaka chaka choyamba cha ulamuliro wa Mfumu Koresi.+