Nehemiya
5 Koma panali amuna ena pamodzi ndi akazi awo amene anayamba kuwadandaula kwambiri Ayuda anzawo.+ 2 Ena ankanena kuti: “Ife ndi ana athu aamuna komanso aakazi tilipo ambiri. Tiyenera kupeza chakudya kuti tikhale ndi moyo.” 3 Ndipo ena ankanena kuti: “Nthawi ya njala, tikumapereka minda yathu ya tirigu, minda yathu ya mpesa ndi nyumba zathu monga chikole kuti tipeze chakudya.” 4 Enanso ankanena kuti: “Ife takongola ndalama kuti tikhome msonkho kwa mfumu wa minda yathu ya tirigu ndi ya mpesa.+ 5 Komatu ife ndi anzathuwo ndife pachibale ndipo ana athu nʼchimodzimodzi ndi ana awo, koma ife tikufunika kusandutsa ana athu aamuna ndi aakazi kukhala akapolo. Ndipo ana athu ena aakazi tawasandutsa kale akapolo.+ Tilibe mphamvu zoti nʼkuletsa zimenezi chifukwa minda yathu ya tirigu ndi ya mpesa ili mʼmanja mwa anthu ena.”
6 Nditamva kudandaula kwawo komanso mawu awowa, ndinakwiya kwambiri. 7 Choncho ndinayamba kuganizira zimenezi mumtima mwanga ndipo ndinapeza kuti anthu olemekezeka ndi atsogoleri anali olakwa. Ndiyeno ndinawauza kuti: “Nonsenu mukuumiriza abale anu kuti akupatseni chiwongoladzanja.”+
Komanso ndinaitanitsa msonkhano waukulu chifukwa cha iwowa. 8 Ndipo ndinawauza kuti: “Ife tayesetsa kuwombola abale athu a Chiyuda amene anagulitsidwa kwa anthu a mitundu ina. Ndiye inu mukugulitsa abale anu+ ndipo mufuna kuti ife tiwawombole?” Atamva zimenezi anangokhala chete, kusowa chonena. 9 Ndiyeno ndinati: “Zimene mukuchitazi si zabwino. Kodi simuyenera kuyenda moopa Mulungu+ kuti adani athu, anthu a mitundu ina, asamatinyoze? 10 Ndiponso ine, abale anga ndi atumiki anga, tikuwakongoza abale athu ndalama ndi chakudya. Chonde, tiyeni tisiye kulandira chiwongoladzanja tikakongoza zinthu.+ 11 Chonde, lero abwezereni minda yawo+ ya tirigu, ya mpesa, ya maolivi, nyumba zawo ndiponso gawo limodzi pa magawo 100 a ndalama, tirigu, vinyo watsopano komanso mafuta zimene munawauza kuti azikupatsani ngati chiwongoladzanja.”
12 Atamva zimenezi anati: “Tiwabwezera ndipo sitiwauzanso kuti atipatse kenakake. Tichita ndendende mmene mwanenera.” Choncho ndinaitana ansembe nʼkulumbiritsa anthuwo kuti achite zimene alonjeza. 13 Komanso ndinakutumula zovala zanga nʼkunena kuti: “Mofanana ndi zimenezi, Mulungu woona akutumule munthu amene sachita zimene walonjeza nʼkumuchotsa mʼnyumba yake ndi pa zinthu zake zonse. Akutumulidwe chonchi nʼkukhala wopanda kanthu.” Ndiyeno gulu lonse la anthulo linati: “Ame!”* Anthuwo anatamanda Yehova ndipo anachita zimene analonjezazo.
14 Komanso kwa zaka 12, kuchokera tsiku limene ndinaikidwa kukhala bwanamkubwa wawo+ mʼdziko la Yuda, kuyambira chaka cha 20+ mpaka chaka cha 32+ cha mfumu Aritasasita,+ ine ndi abale anga sitinadye chakudya choyenera kuperekedwa kwa bwanamkubwa.+ 15 Abwanamkubwa amene analipo ine ndisanakhale, ankalemetsa anthu ndipo tsiku lililonse ankalandira masekeli* 40 asiliva ogulira chakudya ndi vinyo. Komanso atumiki awo ankapondereza anthu. Koma ine sindinachite zimenezo+ chifukwa choopa Mulungu.+
16 Kuwonjezera pamenepo, ndinagwira nawo ntchito yomanga mpandawo ndipo sitinakhale ndi minda.+ Atumiki anga onse anasonkhana kumeneko kuti agwire ntchito. 17 Panali Ayuda ndi atsogoleri okwana 150 amene ankadya nane limodzi komanso anthu a mitundu ina amene anabwera. 18 Ndinauza anthu kuti tsiku lililonse azipha ngʼombe imodzi yamphongo, nkhosa zabwino kwambiri zokwana 6 ndiponso mbalame, ndipo pakatha masiku 10 tinkakhala ndi vinyo wambiri wamtundu uliwonse. Koma sindinapemphe kuti andipatse chakudya choyenera kuperekedwa kwa bwanamkubwa chifukwa anthuwa ankagwira kale ntchito yolemetsa. 19 Mulungu wanga, mundikumbukire pa zonse* zimene ndachitira anthuwa.+