Habakuku
3 Ili ndi pemphero la mneneri Habakuku limene anaimba ngati nyimbo zoimba polira:
2 “Inu Yehova, ndamva uthenga wonena za inu.
Ndachita mantha ndi ntchito zanu, inu Yehova.
Mʼzaka zimenezi* sonyezani ntchito zanu.
Mʼzaka zimenezi chititsani kuti ntchito zanu zidziwike.
Pa nthawi ya mkwiyo wanu kumbukirani kusonyeza chifundo.+
Ulemerero wake unaphimba kumwamba,+
Ndipo dziko lonse linamutamanda.
4 Kuwala kwake kunali ngati kuwala kwa masana.+
Kuwala kwa mitundu iwiri kunkatuluka mʼdzanja lake,
Limene ankabisamo mphamvu zake.
6 Iye anaimirira nʼkugwedeza dziko lapansi.+
Atayangʼana mitundu ya anthu, mitunduyo inadumpha.+
Mapiri akuluakulu omwe adzakhalapo mpaka kalekale anaphwanyidwa,
Ndipo mapiri angʼonoangʼono akalekale anawerama.+
Njira zakalekale ndi zake.
7 Ndinaona mahema a Kusani ali ndi nkhawa.
Nsalu za mahema za ku Midiyani zinanjenjemera.+
Chifukwa munakwera pamahatchi anu,+
Magaleta anu anapambana.+
9 Mwachotsa uta moikamo mwake ndipo ndinu wokonzeka kulasa.
Ndodo* nʼzokonzeka kugwira ntchito yake mogwirizana ndi lumbiro.* (Selah)
Mumagawa dziko lapansi pogwiritsa ntchito mitsinje.
10 Mapiri atakuonani anamva ululu waukulu.+
Mvula yamphamvu inadutsa.
Madzi akuya anachita mkokomo,+
Ndipo anathovokera mʼmwamba.
11 Kumwamba, dzuwa ndi mwezi zinaima.+
Mivi yanu inkayenda ngati kuwala.+
Kungʼanima kwa mkondo wanu kunawala kwambiri.
12 Munadutsa mʼdziko lapansi mutakwiya.
Munapondaponda* mitundu ya anthu mutakwiya.
13 Munapita kukapulumutsa anthu anu, kuti mupulumutse wodzozedwa wanu.
Munaphwanyaphwanya mtsogoleri wa nyumba ya ochimwa.
Nyumba yonseyo inagumulidwa mpaka maziko ake anaonekera. (Selah)
14 Munabaya mitu ya asilikali ake pogwiritsa ntchito zida* zake zomwe,
Pamene iwo ankabwera ngati mphepo yamkuntho kuti adzandiuluze,
Anasangalala kwambiri kumeza munthu wosautsidwa amene anamubisalira.
15 Munadutsa panyanja ndi mahatchi anu.
Munadutsa pamadzi ambiri.
16 Nditamva mawu ake, mʼmimba mwanga munabwadamuka.
Ndipo milomo yanga inanjenjemera.
Mafupa anga anayamba kuwola,+
Ndipo miyendo yanga inanjenjemera.
Koma ndikuyembekezera mofatsa tsiku la masautso.+
Chifukwa likubwera kwa anthu amene amatiukira.
17 Ngakhale mtengo wa mkuyu usachite maluwa,
Mtengo wa mpesa usabale zipatso,
Mtengo wa maolivi usabereke,
Minda* isatipatse chakudya,
Nkhosa ndi ngʼombe zithemo mʼkhola,
18 Ine ndidzakhalabe wosangalala chifukwa cha Yehova,
Ndipo ndidzasangalala chifukwa cha Mulungu wachipulumutso changa.+
19 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndi amene amandipatsa mphamvu.+
Iye adzachititsa kuti miyendo yanga ikhale ngati ya mbawala,
Komanso kuti ndiponde pamalo okwera.”+
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo zanga za zingwe.