Machitidwe a Atumwi
27 Ulendo wathu wapamadzi wopita ku Italy+ utatsimikizika, Paulo ndi akaidi ena anaperekedwa mʼmanja mwa mtsogoleri wa asilikali dzina lake Yuliyo, wamʼgulu la asilikali la Augusito. 2 Ku Adiramutiyo tinakwera ngalawa imene inali itatsala pangʼono kunyamuka ulendo wopita kumadoko amʼmbali mwa nyanja mʼchigawo cha Asia. Kenako tinanyamuka limodzi ndi Arisitako,+ yemwe anali wa ku Makedoniya ku Tesalonika. 3 Tsiku lotsatira tinafika ku Sidoni, ndipo Yuliyo anakomera mtima Paulo moti anamulola kupita kwa anzake kuti akamusamalire.
4 Titalowanso panyanja kuchokera kumeneko, tinayenda mʼmbali mwa chilumba cha Kupuro chimene chinkatiteteza ku mphepo imene inkawomba kuchokera kumene ife tinkapita. 5 Tinayenda panyanja molambalala Kilikiya ndi Pamfuliya ndipo tinafika padoko la Mura, ku Lukiya. 6 Kumeneko mtsogoleri wa asilikali anapeza ngalawa yochokera ku Alekizandiriya yomwe inkapita ku Italy ndipo anatikweza mmenemo. 7 Choncho tinayenda pangʼonopangʼono kwa masiku angapo ndipo tinafika ku Kinido movutikira. Chifukwa cha mphepo yomwe inkawomba kuchokera kutsogolo kwathu, tinadzera ku Salimone kuti chilumba cha Kerete chizititeteza ku mphepoyo. 8 Titayenda movutikira mʼmbali mwa chilumba chimenechi, tinafika pamalo ena otchedwa Madoko Okoma, amene anali pafupi ndi mzinda wa Laseya.
9 Tsopano panali patapita nthawi yaitali, ndipo kuyenda panyanja kunali koopsa chifukwa ngakhale nthawi ya kusala kudya kwa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo+ inali itadutsa kale. Choncho Paulo anawapatsa malangizo. 10 Iye anawauza kuti: “Anthu inu, ndikuona kuti ulendowu tikauyamba panopa tiwonongetsa zambiri. Tiwonongetsa katundu ndiponso ngalawa, ngakhalenso miyoyo yathu.” 11 Koma mtsogoleri wa asilikali anamvera woyendetsa ngalawa ndi mwiniwake wa ngalawayo mʼmalo momvera zimene Paulo ananena. 12 Popeza dokolo silinali labwino kukhalapo nthawi yozizira, anthu ambiri anagwirizana ndi zoti achokepo. Iwo ankafuna kuona ngati nʼzotheka kukafika ku Finikesi kuti akakhale kumeneko nthawi yozizira. Finikesi linali doko la Kerete loyangʼana kumpoto chakumʼmawa ndi kumʼmwera chakumʼmawa.
13 Mphepo yakumʼmwera itayamba kuwomba pangʼonopangʼono, anaganiza kuti zimene ankafuna zitheka. Choncho anakweza nangula nʼkuyamba kuyenda mʼmbali mwa chilumba cha Kerete. 14 Koma pasanapite nthawi, mphepo yamkuntho yotchedwa Yulakilo* inayamba kuwomba ngalawayo. 15 Popeza ngalawa inkawombedwa ndi mphepo yamphamvu ndipo sitinathe kuiwongolera kuti iyende moyangʼana kumene mphepoyo inkachokera, tinagonja ndipo tinatengedwa nayo. 16 Kenako tinayamba kuyenda mʼmbali mwa chilumba china chachingʼono chotchedwa Kauda chimene chinkatiteteza ku mphepo. Komabe tinkalephera kuwongolera bwato lalingʼono limene ngalawayo inkakoka. 17 Ndiyeno atakweza bwatolo mʼngalawa, anayamba kumanga ngalawayo ndi zomangira kuti ilimbe. Ndipo poopa kuti ngalawayo ingatitimire mumchenga ku Suriti,* iwo anatsitsa zingwe zomangira chinsalu cha ngalawa moti inkakankhidwa ndi mphepo. 18 Koma popeza mphepo yamkuntho inkatiwomba ndiponso kutikankha mwamphamvu, tsiku lotsatira anthu anayamba kutaya katundu kuti ngalawa ipepukidwe. 19 Tsiku lachitatu, anataya zingwe zokwezera chinsalu cha ngalawayo.
20 Titaona kuti dzuwa komanso nyenyezi sizinaoneke kwa masiku ambiri komanso tikukankhidwa ndi chimphepo champhamvu, tinayamba kukayikira zoti tipulumuka. 21 Anthuwo atakhala nthawi yaitali osadya kanthu, Paulo anaima pakati pawo nʼkunena kuti: “Anthu inu, mukanamvera malangizo anga, osachoka ku Kerete kuja, sitikanavutika chonchi komanso katundu sakanawonongeka.+ 22 Komabe musadandaule chifukwa palibe amene ataye moyo wake, koma ngalawa yokhayi iwonongeka. 23 Usiku wapitawu mngelo+ wa Mulungu wanga amene ndikumuchitira utumiki wopatulika, anaima pafupi ndi ine 24 nʼkunena kuti: ‘Usaope Paulo. Uyenera kukaima pamaso pa Kaisara.+ Ndipo dziwa kuti chifukwa cha iwe, Mulungu apulumutsa anthu onse amene uli nawo pa ulendowu.’ 25 Choncho limbani mtima anthu inu, chifukwa ndikukhulupirira kuti Mulungu achita zonse zimene wandiuza. 26 Komabe, ngalawa yathuyi iwonongeka pafupi ndi chilumba chinachake.”+
27 Pa usiku wa 14, mphepo inayamba kutikankhira uku ndi uku panyanja ya Adiriya. Ndiyeno pakati pa usiku, oyendetsa ngalawayo anayamba kuganiza kuti akuyandikira kumtunda. 28 Choncho anayeza kuzama kwa nyanja nʼkupeza kuti inali mamita 36. Atayenda kamtunda pangʼono anayezanso kuzama kwake nʼkupeza mamita 27. 29 Koma poopa kuti tiwomba miyala, anatsitsa anangula 4 kumbuyo kwa ngalawayo ndipo ankalakalaka kutangocha. 30 Tsopano oyendetsa ngalawayo ankafuna kuthawamo. Choncho anatsitsira bwato lija panyanja ponamizira kuti akufuna kutsitsa anangula kutsogolo kwa ngalawayo. 31 Paulo anauza mtsogoleri wa asilikali ndi asilikaliwo kuti: “Anthu awa akachoka mʼngalawa muno, simupulumuka.”+ 32 Kenako asilikaliwo anadula zingwe za bwatolo nʼkulisiya kuti lipite.
33 Kutatsala pangʼono kucha, Paulo anayamba kuuza onse kuti adye. Iye anati: “Tsopano patha masiku 14 mukudikirira komanso muli ndi nkhawa ndipo simunadye chilichonse. 34 Choncho ndikukulimbikitsani kuti mudye kuti zinthu zikuyendereni bwino. Chifukwa ngakhale tsitsi limodzi lamʼmutu mwanu siliwonongeka.” 35 Atanena zimenezi, anatenga mkate. Kenako anayamika Mulungu pamaso pa onse nʼkugawagawa mkatewo ndipo iye anayamba kudya. 36 Atatero, onse analimba mtima nʼkuyamba kudya. 37 Tonse pamodzi, mʼngalawamo tinalimo anthu 276. 38 Onse atadya nʼkukhuta, anatayira tirigu mʼnyanja kuti ngalawayo ipepukidwe.+
39 Kutacha, sanadziwe kuti ali kuti,+ koma anaona gombe linalake lamchenga ndipo ankafunitsitsa kuti ngati nʼkotheka akaimitse ngalawa pamenepo. 40 Choncho anadula zingwe za anangula nʼkuzigwetsera mʼnyanja. Anamasulanso zingwe zomangira nkhafi zowongolera. Atakweza mʼmwamba nsalu yakutsogolo ya ngalawa, anayamba kulowera kugombelo. 41 Kenako anafika pachimulu cha mchenga chomwe mafunde ankachiwomba mbali zonse. Kutsogolo kwa ngalawayo kunakanirira pansi mumchengawo osasunthika ndipo mafunde amphamvu anayamba kuwomba kumbuyo kwake moti inayamba kusweka zidutswazidutswa. 42 Zitatero asilikali anaganiza zopha akaidi kuti pasapezeke aliyense wosambira nʼkuthawa.+ 43 Koma mtsogoleri wa asilikali ankafunitsitsa kuti Paulo akafike naye ali bwinobwino, choncho anawaletsa kuchita zimene ankafunazo. Ndiyeno analamula odziwa kusambira kuti alumphire mʼnyanjamo kuti akhale oyamba kukafika kumtunda. 44 Analamulanso ena onse kuti achite chimodzimodzi, ena pamatabwa ndipo ena pa zidutswa za ngalawayo. Pamapeto pake onse anafika kumtunda ali bwinobwino.+