1 Mbiri
5 Ana a Yafeti anali Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala,+ Meseki+ ndi Tirasi.+
6 Ana a Gomeri anali Asikenazi, Rifati ndi Togarima.+
7 Ana a Yavani anali Elisha, Tarisi, Kitimu ndi Rodanimu.
8 Ana a Hamu anali Kusi,+ Miziraimu, Puti ndi Kanani.+
9 Ana a Kusi anali Seba,+ Havila, Sabita, Raama+ ndi Sabiteka.
Ana a Raama anali Sheba ndi Dedani.+
10 Kusi anabereka Nimurodi,+ amene anali woyamba kukhala wamphamvu padziko lapansi.
11 Miziraimu anabereka Ludimu,+ Anamimu, Lehabimu, Nafituhimu,+ 12 Patirusimu,+ Kasiluhimu (Afilisiti+ anachokera mwa iyeyu) ndiponso Kafitorimu.+
13 Kanani anabereka Sidoni+ mwana wake woyamba kenako anabereka Heti.+ 14 Analinso kholo la Ayebusi,+ Aamori,+ Agirigasi,+ 15 Ahivi,+ Aariki, Asini, 16 Aarivadi,+ Azemari ndi Ahamati.
18 Aripakisadi anabereka Shela+ ndipo Shela anabereka Ebere.
19 Ebere anabereka ana awiri. Wina dzina lake anali Pelegi,*+ chifukwa mʼmasiku ake dziko* lapansi linagawanika. Mʼbale wakeyo dzina lake anali Yokitani.
20 Yokitani anabereka Alamodadi, Selefi, Hazaramaveti, Yera,+ 21 Hadoramu, Uzali, Dikila, 22 Obali, Abimaele, Sheba, 23 Ofiri,+ Havila+ ndi Yobabi. Onsewa anali ana a Yokitani.
28 Ana a Abulahamu anali Isaki+ ndi Isimaeli.+
29 Mabanja awo anali awa: Nebayoti,+ mwana woyamba wa Isimaeli. Kedara,+ Adibeele, Mibisamu,+ 30 Misima, Duma, Maasa, Hadadi, Tema, 31 Yeturi, Nafisi ndi Kedema. Amenewa anali ana a Isimaeli.
32 Ana amene Ketura+ mkazi wamngʼono* wa Abulahamu anabereka, anali Zimirani, Yokesani, Medani, Midiyani,+ Isibaki ndi Shuwa.+
Ana a Yokesani anali Sheba ndi Dedani.+
33 Ana a Midiyani anali Efa,+ Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida.
Onsewa anali ana aamuna a Ketura.
34 Abulahamu anabereka Isaki.+ Ana a Isaki anali Esau+ ndi Isiraeli.+
35 Ana a Esau anali Elifazi, Reueli, Yeusi, Yalamu ndi Kora.+
36 Ana a Elifazi anali Temani,+ Omari, Zefo, Gatamu, Kenazi, Timina ndi Amaleki.+
37 Ana a Reueli anali Nahati, Zera, Shama ndi Miza.+
38 Ana a Seiri+ anali Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, Disoni, Ezeri ndi Disani.+
39 Ana a Lotani anali Hori ndi Homamu. Mchemwali wake wa Lotani anali Timina.+
40 Ana a Sobala anali Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu.
Ana a Zibeoni anali Aya ndi Ana.+
41 Mwana* wa Ana anali Disoni.
Ana a Disoni anali Hemadani, Esibani, Itirani ndi Kerana.+
42 Ana a Ezeri+ anali Bilihani, Zavani ndi Ekani.
Ana a Disani anali Uzi ndi Arani.+
43 Mafumu amene analamulira dziko la Edomu,+ Aisiraeli* asanayambe kulamulidwa ndi mfumu ina iliyonse,+ ndi awa: Bela mwana wa Beori. Dzina la mzinda wake linali Dinihaba. 44 Bela atamwalira, Yobabi mwana wa Zera wa ku Bozira,+ anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 45 Yobabi atamwalira, Husamu wa ku Temani, anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 46 Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdera la Mowabu, anayamba kulamulira mʼmalo mwake. Dzina la mzinda wake linali Aviti. 47 Hadadi atamwalira, Samila wa ku Masereka anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 48 Samila atamwalira, Shauli wamumzinda wa Rehoboti, womwe unali mʼmbali mwa Mtsinje,* anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 49 Shauli atamwalira, Baala-hanani mwana wa Akibori anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 50 Baala-hanani atamwalira, Hadadi anayamba kulamulira mʼmalo mwake. Dzina la mzinda wake linali Pau ndipo mkazi wake dzina lake linali Mehetabele mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Mezahabu. 51 Kenako Hadadi anamwalira.
Mafumu a Edomu anali Mfumu Timina, Mfumu Aliva, Mfumu Yeteti,+ 52 Mfumu Oholibama, Mfumu Ela, Mfumu Pinoni, 53 Mfumu Kenazi, Mfumu Temani, Mfumu Mibezari, 54 Mfumu Magidieli ndi mfumu Iramu. Amenewa anali mafumu a Edomu.