2 Mafumu
14 Mʼchaka chachiwiri cha Yehoasi+ mwana wa Yehoahazi mfumu ya Isiraeli, Amaziya mwana wa Yehoasi mfumu ya Yuda, anakhala mfumu. 2 Amaziya anali ndi zaka 25 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 29. Mayi ake anali a ku Yerusalemu ndipo dzina lawo linali Yehoadini.+ 3 Iye anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova, koma osati ngati Davide+ kholo lake. Anachita zonse ngati mmene Yehoasi bambo ake anachitira.+ 4 Koma sanachotse malo okwezeka+ ndipo anthu ankaperekabe nsembe zautsi ndi nsembe zina mʼmalo okwezekawo.+ 5 Ndiyeno ufumu wakewo utangokhazikika, anapha atumiki ake amene anapha bambo ake, omwe anali mfumu.+ 6 Koma ana a anthu omwe anapha bambo akewo sanawaphe, mogwirizana ndi lamulo la Yehova lomwe linalembedwa mʼChilamulo cha Mose lakuti: “Abambo asamaphedwe chifukwa cha zimene ana awo achita ndipo ana asamaphedwe chifukwa cha zimene abambo awo achita. Munthu aliyense aziphedwa chifukwa cha tchimo lake.”+ 7 Amaziya anapha Aedomu+ okwana 10,000 mʼchigwa cha Mchere+ nʼkulanda mzinda wa Sela pa nkhondo.+ Mzindawo anaupatsa dzina lakuti Yokiteeli ndipo dzina lake ndi lomweli mpaka lero.
8 Kenako Amaziya anatumiza anthu kwa Yehoasi mwana wa Yehoahazi mwana wa Yehu mfumu ya Isiraeli, kukamuuza kuti: “Bwera tidzamenyane.”+ 9 Yehoasi mfumu ya Isiraeli atamva anayankha Amaziya mfumu ya Yuda kuti: “Chitsamba chaminga cha ku Lebanoni chinatumiza uthenga kwa mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni wakuti, ‘Ndipatse mwana wako wamkazi kuti mwana wanga wamwamuna amukwatire.’ Koma nyama yakutchire ya ku Lebanoni inadutsa pamenepo nʼkupondaponda chitsamba chamingacho. 10 Chifukwa chakuti wagonjetsa Edomu,+ wayamba kukula mtima. Sangalala ndi ulemerero umene wapeza ndipo khala mʼnyumba* mwako momwemo. Nʼchifukwa chiyani ukuputa tsoka chonsecho iwe ndi Ayudawo mugonja?” 11 Koma Amaziya sanamvere.+
Choncho Yehoasi, mfumu ya Isiraeli, anapitadi ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anakumana nʼkuyamba kumenyana ku Beti-semesi+ mʼdziko la Yuda.+ 12 Pa nkhondoyo, Ayuda anagonjetsedwa ndi Aisiraeli moti aliyense anathawira kunyumba* kwake. 13 Yehoasi mfumu ya Isiraeli anagwira Amaziya mfumu ya Yuda mwana wa Yehoasi, mwana wa Ahaziya ku Beti-semesiko. Kenako Yehoasi anatenga Amaziya nʼkupita naye ku Yerusalemu ndipo anakagumula mpanda wa Yerusalemu kuyambira pa Geti la Efuraimu+ mpaka pa Geti la Pakona.+ Anagumula mpata waukulu pafupifupi mamita 178.* 14 Yehoasi anatenga golide ndi siliva yense komanso ziwiya zonse zimene anazipeza panyumba ya Yehova ndi mʼnyumba yosungiramo chuma cha mfumu. Anagwiranso anthu ena ndipo kenako anabwerera ku Samariya.
15 Nkhani zina zokhudza Yehoasi, zimene anachita, mphamvu zake komanso mmene anamenyanirana ndi Amaziya mfumu ya Yuda, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli. 16 Kenako Yehoasi, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda ku Samariya+ pamodzi ndi mafumu a Isiraeli. Ndiyeno Yerobowamu*+ mwana wake anakhala mfumu mʼmalo mwake.
17 Amaziya+ mwana wa Yehoasi mfumu ya Yuda, anakhalabe ndi moyo zaka 15 pambuyo pa imfa ya Yehoasi+ mwana wa Yehoahazi mfumu ya Isiraeli.+ 18 Nkhani zina zokhudza Amaziya zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda. 19 Patapita nthawi, anthu ena anamukonzera chiwembu+ ku Yerusalemu, choncho iye anathawira ku Lakisi. Koma anthuwo anatumiza anthu ena omwe anamutsatira ku Lakisiko nʼkukamuphera komweko. 20 Atatero anamunyamula pamahatchi nʼkukamuika mʼmanda a makolo ake ku Yerusalemu mu Mzinda wa Davide.+ 21 Kenako anthu onse a ku Yuda anatenga Azariya,*+ yemwe pa nthawiyo anali ndi zaka 16,+ nʼkumuika kuti akhale mfumu mʼmalo mwa bambo ake Amaziya.+ 22 Mfumuyo,* mofanana ndi makolo ake, itamwalira, Azariya anamanganso mzinda wa Elati+ nʼkuubwezera ku Yuda.+
23 Mʼchaka cha 15 cha Amaziya mwana wa Yehoasi mfumu ya Yuda, Yerobowamu+ mwana wa Yehoasi mfumu ya Isiraeli anakhala mfumu ku Samariya ndipo analamulira zaka 41. 24 Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova. Sanasiye kuchita machimo onse amene Aisiraeli ankachita chifukwa cha Yerobowamu mwana wa Nebati.+ 25 Yerobowamu anabwezeretsa malire a Isiraeli kuyambira ku Lebo-hamati*+ mpaka kunyanja ya Araba.*+ Anachita zimenezi mogwirizana ndi mawu a Yehova Mulungu wa Isiraeli omwe anawalankhula kudzera mwa mtumiki wake Yona+ mwana wa Amitai, mneneri wa ku Gati-heferi.+ 26 Yehova anali ataona mavuto aakulu omwe Aisiraeli ankakumana nawo.+ Kunalibe aliyense woti akanawathandiza, ngakhale wooneka wonyozeka ndi wofooka. 27 Koma Yehova analonjeza kuti sadzachotseratu dzina la Isiraeli padziko lapansi,+ choncho anawapulumutsa ndi dzanja la Yerobowamu mwana wa Yehoasi.+
28 Nkhani zina zokhudza Yerobowamu, zonse zimene anachita, mphamvu zake, mmene anamenyera nkhondo komanso mmene anabwezeretsera Damasiko+ ndi Hamati+ ku Yuda mu Isiraeli, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli. 29 Kenako Yerobowamu, mofanana ndi makolo ake, anamwalira nʼkuikidwa mʼmanda pamodzi ndi mafumu a Isiraeli ndipo mwana wake Zekariya+ anakhala mfumu mʼmalo mwake.