2 Mafumu
2 Yehova atatsala pangʼono kutenga Eliya+ mumphepo yamkuntho kupita naye kumwamba,*+ Eliya ndi Elisa+ ananyamuka ku Giligala.+ 2 Kenako Eliya anauza Elisa kuti: “Iweyo utsale kuno, chifukwa Yehova wandituma ku Beteli.” Koma Elisa anati: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo ndiponso inu muli apa, sindikusiyani.” Choncho iwo anapita ku Beteli.+ 3 Ndiyeno ana a aneneri* amene anali ku Beteli anabwera kwa Elisa nʼkumufunsa kuti: “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova atenga mbuye wako kuti asakhalenso mtsogoleri wako?”+ Iye anayankha kuti: “Ndikudziwa zimenezo. Khalani chete.”
4 Kenako Eliya anauza Elisa kuti: “Elisa, utsale kuno chifukwa Yehova wandituma ku Yeriko.”+ Koma Elisa anayankha kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo ndiponso inu muli apa, sindikusiyani.” Choncho iwo anafika ku Yeriko. 5 Kenako ana a aneneri amene anali ku Yeriko anapita kwa Elisa nʼkumufunsa kuti: “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova atenga mbuye wako kuti asakhalenso mtsogoleri wako?” Iye anayankha kuti: “Ndikudziwa zimenezo. Khalani chete.”
6 Ndiyeno Eliya anauza Elisa kuti: “Iweyo utsale kuno, chifukwa Yehova wandituma ku Yorodano.” Koma Elisa anayankha kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo ndiponso inu muli apa, sindikusiyani.” Choncho iwo anapitiriza ulendo wawo. 7 Ndiyeno ana a aneneri okwana 50 anaima chapatali nʼkumawayangʼana. Koma Eliya ndi Elisa anaima pafupi ndi mtsinje wa Yorodano. 8 Kenako Eliya anatenga chovala chake chauneneri+ ndipo anachipinda nʼkumenya madzi a mumtsinjewo. Madziwo anagawanika uku ndi uku moti iwo anawoloka pouma.+
9 Iwo atangowoloka, Eliya anauza Elisa kuti: “Pempha chimene ukufuna kuti ndikuchitire ndisanatengedwe nʼkukusiya.” Elisa anati: “Chonde, ndilandire magawo awiri+ a mzimu wanu.”+ 10 Eliya anati: “Wapempha chinthu chovuta. Ukandiona ndikutengedwa, zimene wapemphazi zikuchitikiradi, koma ukapanda kundiona, sizichitika.”
11 Pamene ankayenda, uku akulankhulana, anangoona galeta* lankhondo lowala ngati moto ndi mahatchi* owala ngati moto.+ Galeta ndi mahatchiwo zinadutsa pakati pawo nʼkuwalekanitsa ndipo Eliya anatengedwa mumphepo yamkuntho nʼkupita kumwamba.*+ 12 Elisa ankaona zonse zimene zinkachitikazo ndipo ankafuula kuti: “Bambo anga ine! Bambo anga ine! Galeta lankhondo la Isiraeli ndi okwera mahatchi ake!”+ Elisa ataona kuti Eliya wapita, anagwira zovala zake nʼkuzingʼamba pakati.+ 13 Atatero anatola chovala chauneneri+ cha Eliya chimene chinagwa pansi ndipo anabwerera nʼkukaima mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodano. 14 Kenako anatenga chovala chauneneri cha Eliya chimene chinagwa chija nʼkumenya madzi amumtsinjewo ndipo anati: “Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya?” Atatero madziwo anagawanika ndipo Elisa anawoloka.+
15 Ana a aneneri amene anali ku Yeriko atamuona chapatali, ananena kuti: “Tsopano mzimu umene unali ndi Eliya uli ndi Elisa.”+ Choncho anapita kukakumana naye ndipo anamugwadira mpaka nkhope zawo kufika pansi. 16 Ndiyeno ana a aneneriwo anauza Elisa kuti: “Ife atumiki anu tili ndi amuna 50 amphamvu. Bwanji tiwatume kukafunafuna mbuye wanu? Mwina mzimu* wa Yehova wamunyamula ndipo wamʼponya paphiri linalake kapena mʼchigwa.”+ Koma Elisa anayankha kuti: “Ayi musawatume.” 17 Koma iwo anamʼkakamiza mpaka iye anachita manyazi, moti anati: “Atumeni.” Choncho anatuma amuna 50 ndipo anamufufuza kwa masiku atatu koma sanamʼpeze. 18 Anthuwo atabwerera kwa Elisa ku Yeriko,+ Elisa ananena kuti: “Pajatu ndinakuuzani kuti musapite.”
19 Patapita nthawi, anthu amumzindawo anauza Elisa kuti: “Inu mbuyathu mukudziwa kuti mzindawu uli pamalo abwino,+ koma madzi ake ndi oipa ndipo nthaka ndi yosabereka.”* 20 Elisa atamva zimenezi ananena kuti: “Ndibweretsereni kambale katsopano kolowa ndipo muikemo mchere.” Anthuwo anamʼbweretseradi. 21 Ndiyeno Elisa anapita pamene panayambira madziwo nʼkuponyapo mchere uja+ nʼkunena kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ndakonza madziwa kuti akhale abwino ndipo sadzachititsanso imfa kapena kusabereka.’”* 22 Madziwo ndi abwino mpaka lero mogwirizana ndi zimene Elisa ananena.
23 Kenako Elisa ananyamuka nʼkumapita ku Beteli. Ali mʼnjira, anyamata ena a mumzindawo anayamba kumunyoza+ kuti: “Choka kuno wadazi iwe! Choka kuno wadazi iwe!” 24 Kenako Elisa anatembenuka nʼkuwayangʼana ndipo anawatemberera mʼdzina la Yehova. Ndiyeno zimbalangondo+ ziwiri zazikazi zinatuluka patchire nʼkukhadzula anyamata 42.+ 25 Elisa anapitiriza ulendo wake ndipo anakafika kuphiri la Karimeli.+ Atachoka kumeneko anabwerera ku Samariya.