Ekisodo
5 Kenako Mose ndi Aroni anapita kwa Farao nʼkumuuza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Lola anthu anga apite mʼchipululu kuti akachite chikondwerero.’” 2 Koma Farao anati: “Yehova ndi ndani+ kuti ndimvere mawu ake nʼkulola Aisiraeli kuti apite?+ Ine sindikumudziwa Yehova ngakhale pangʼono ndipo sindilola kuti Aisiraeli apite.”+ 3 Komabe iwo anati: “Mulungu wa Aheberi walankhula nafe. Ndiye mutilole chonde, tipite ulendo wamasiku atatu mʼchipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.+ Ngati sititero, adzatipha ndi matenda kapena lupanga.” 4 Mfumu ya Iguputo inawayankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani iwe Mose ndi Aroni mukufuna kuti anthu asiye ntchito zawo? Bwererani ku ntchito yanu!”*+ 5 Farao anapitiriza kuti: “Anthu amenewa ndi ambiri mʼdziko lino, ndipo inu mukufuna kusokoneza ntchito yawo.”
6 Tsiku lomwelo Farao analamula amene ankawayangʼanira komanso akapitawo awo kuti: 7 “Anthu amenewa musawapatsenso udzu woumbira njerwa.+ Muwasiye azikafuna okha udzu umenewo. 8 Koma muwauze kuti chiwerengero cha njerwa zofunika chikhala chakale chomwe chija. Musawachepetsere chiwerengerocho, chifukwa ayamba ulesi. Nʼchifukwa chake akulira kuti, ‘Tikufuna tipite kukapereka nsembe kwa Mulungu wathu!’ 9 Agwiritseni ntchito yakalavulagaga anthu amenewa ndipo muwapatse ntchito yambiri kuti asamvere zabodza.”
10 Choncho amene ankawayangʼanira+ komanso akapitawo awo anapita kwa Aisiraeliwo nʼkukawauza kuti: “Mverani zimene Farao wanena, ‘Sindikupatsaninso udzu woumbira njerwa. 11 Muzipita nokha kukafuna udzu kulikonse kumene mungaupeze, koma ntchito yanu sichepetsedwa ngakhale pangʼono.’” 12 Chotero, anthu anali balalabalala mʼdziko lonse la Iguputo kukafuna mapesi mʼmalo mwa udzu. 13 Choncho amene ankawayangʼanira aja ankawakakamiza kugwira ntchito ponena kuti: “Aliyense azimaliza ntchito yake tsiku lililonse ngati mmene munkachitira pamene tinkakupatsani udzu.” 14 Kenako oyangʼanira ntchito a Farao anamenya+ akapitawo a Aisiraeli amene iwo anawaika nʼkuwafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani dzulo ndi lero simunamalize kuumba njerwa zimene munauzidwa ngati mmene munkachitira poyamba?”
15 Zitatero akapitawo a Aisiraeli anapita kwa Farao nʼkukamudandaulira kuti: “Nʼchifukwa chiyani atumiki anu mukuwachitira zimenezi? 16 Ife atumiki anu sitikupatsidwa udzu, koma akutiuza kuti, ‘Umbani njerwa!’ ndipo tikumenyedwa ngakhale kuti olakwa ndi anthu anu.” 17 Koma iye anati: “Mukuchita ulesi, mukuchita ulesi!+ Nʼchifukwa chake mukunena kuti, ‘Tikufuna tipite kukapereka nsembe kwa Yehova.’+ 18 Choncho pitani, kagwireni ntchito! Simuzipatsidwanso udzu, koma chiwerengero cha njerwa zimene muziumba sichisintha.”
19 Pamenepo akapitawo a Aisiraeli anaona kuti zinthu zawaipira kwambiri chifukwa cha zimene anauzidwa kuti: “Musachepetse ngakhale pangʼono chiwerengero cha njerwa zimene aliyense akuyenera kuumba tsiku lililonse.” 20 Zitatero akapitawowa anakumana ndi Mose ndi Aroni, amene ankawadikira kuti aonane nawo pamene amachokera kwa Farao. 21 Nthawi yomweyo iwo anati: “Yehova aone zimene mwachitazi ndipo akuweruzeni chifukwa mwachititsa kuti Farao ndi atumiki ake aipidwe nafe,* moti mwawapatsa lupanga mʼmanja mwawo kuti atiphe.”+ 22 Pamenepo Mose anatembenukira kwa Yehova nʼkunena kuti: “Yehova, nʼchifukwa chiyani mwalola kuti anthuwa azunzike? Nʼchifukwa chiyani munandituma? 23 Kuchokera pamene ndinapita kukalankhula ndi Farao mʼdzina lanu,+ iye wachitira anthu awa zinthu zoipa kwambiri,+ ndipo inu simunapulumutse anthu anu.”+