Nyimbo ya Asafu.+
82 Mulungu waima pamsonkhano wake,+
Akuweruza pakati pa milungu kuti:+
2 “Kodi mupitiriza kuweruza mopanda chilungamo+
Komanso kukondera anthu oipa mpaka liti?+ (Selah)
3 Tetezani anthu onyozeka ndi ana amasiye.+
Chitirani chilungamo anthu amene alibe wowathandiza komanso osauka.+
4 Pulumutsani munthu wonyozeka ndi wosauka.
Alanditseni mʼmanja mwa anthu oipa.”
5 Milunguyo sikudziwa kapena kuzindikira.+
Ikuyendayenda mumdima,
Maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.+
6 “Ine ndanena kuti, ‘Inu ndinu milungu,+
Nonsenu ndinu ana a Wamʼmwambamwamba.
7 Koma mudzafa ngati mmene anthu onse amafera.+
Ndipo mudzagwa ngati mmene kalonga aliyense amagwera!’”+
8 Nyamukani inu Mulungu, ndipo muweruze dziko lapansi,+
Chifukwa mitundu yonse ya anthu ndi yanu.